bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 7
Isaiah 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 8 →
1
Pamene Ahazi, mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya, anali mfumu ya ku Yuda, Rezini mfumu ya ku Siriya ndiponso Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya ku Israele, adaadza ku Yerusalemu, kuti adzathire nkhondo mzindawo, koma sadaugonjetse.
2
Banja lachifumu la ku Yuda litamva kuti dziko la Siriya lagwirizana ndi la Efuremu, mfumu pamodzi ndi anthu ake omwe adanjenjemera, monga m'mene mitengo yam'nkhalango imagwedezekera ndi mphepo.
3
Tsono Chauta adauza Yesaya kuti, “Tenga mwana wako Seari-Yasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku Munda wa Mmisiri Woyeretsa nsalu.
4
Ukamuuze kuti achenjere, akhale phee, asaope, ndipo mtima wake usafooke chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi dziko lake la Siriya ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. Ameneŵa ali ngati zongofuka moto.
5
Mfumu ya ku Siriya ndi mfumu ya ku Efuremu apangana kuti akuchiteni choipa. Akunena kuti,
6
‘Tiyeni tikalimbane ndi dziko la Yuda, tikaliwopse. Tikaligonjetse kuti likhale lathu, ndipo tikalonge ufumu mwana wa Tabeele kumeneko.’
7
“Komabe zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi, akuti, ‘Zimenezo sizidzatheka, sizidzachitika konse.
8
Paja dziko la Siriya limagonera pa likulu lake Damasiko, ndipo Damasiko amagonera pa mfumu yake Rezini. Kunena za Aefuremu, zisanapite zaka 65, adzaonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.
9
Dziko la Efuremu limagonera pa likulu lake Samariya, ndipo Samariya amagonera pa mfumu yake Peka. Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu, ndithu simudzalimba konse.’ ”
10
Chauta adalankhulanso ndi Ahazi kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
11
“Upemphe chizindikiro kwa Chauta, Mulungu wako. Chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”
12
Koma Ahazi adati, “Sindidzapempha, ndipo sindidzayesa Chauta ai.”
13
Apo Yesaya adati, “Mumve tsono, inu chidzukulu cha Davide! Kodi sikukukukwanirani kutopetsa anthu, apa mufuna kutopetsa ndi Mulungu wanga yemwe?
14
Nchifukwa chake Ambuye omwe adzakupatsani inu chizindikiro. Onani, namwali uja watenga pathupi ndipo adzabala mwana wamwamuna, mwanayo adzamutcha dzina lake Imanuele.
15
Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziŵa kukana choipa ndi kusankha chabwino.
16
Koma nthaŵi imeneyo isanafike, maiko a mafumu aŵiri amene akukuwopsaniwo, adzakhala atasanduka mabwinja.
17
“Chauta adzafikitsa pa inu, pa anthu anu, ndiponso pa banja la bambo wanu, masiku amavuto oti sadakhalepo kuyambira tsiku limene Efuremu adapatukana ndi Yuda. Ndiye kuti adzafikitsa mfumu ya ku Asiriya.”
18
“Tsiku limenelo Chauta adzalizira khweru Aejipito ndipo adzabwera ambiri ngati ntchentche, zochokera ku mathero a nthambi za mtsinje wa Nailo. Adzaliziranso Aasiriya ndipo adzabwera ambiri ngati njuchi.
19
Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika m'zigwa zozama, m'ming'alu yam'matanthwe ndi pa zitsamba zonse zaminga, ndiponso pa mabusa onse.
20
“Tsiku limenelo Ambuye adzalemba wometa wochokera ku tsidya la mtsinje wa Yufurate, ndiye kuti mfumu ya ku Asiriya. Ndi lumo lake adzakumetani tsitsi lakumutu ndi lam'thupi, ndi ndevu zomwe.
21
“Tsiku limenelo mwina munthu adzangosunga ng'ombe yaing'ono yamkaka ndi mbuzi ziŵiri.
22
Komabe adzapeza ndithu mkaka wochuluka, mwakuti munthuyo azidzadya bwino kwambiri. Pakuti aliyense amene adzatsalire m'dzikomo azidzadya chambiko ndiponso uchi.
23
“Tsiku limenelo likadzafika, minda yamphesa yabwino, yomwe ili ndi mitengo yokwana chikwi m'munda uliwonse ndipo mtengo wake ndi masekeli siliva okwana chikwi chimodzi pa mtengo uliwonse, mudzamera a mkandankhuku ndi minga.
24
Anthu adzafika kumeneko kudzachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti m'dziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga.
25
Ndipo m'mapiri monse m'mene kale munkalimidwa, anthu sadzafikako, kuwopa mkandankhukuwo ndi mingayo. Malowo adzasanduka odyetserako ng'ombe ndi nkhosa basi.”
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66