bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 30
Isaiah 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 31 →
1
Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira.
2
Amapita ku Ejipito kukapempha chithandizo, Ine osandifunsa. Amathaŵira kwa Farao kuti aŵatchinjirize, amakafuna malo opulumukirako ku Ejipito.
3
Koma kutchinjiriza kwa Farao kudzakuchititsani manyazi, ndipo malo opulumukirako a ku Ejipitowo mudzachita nawo manyazi.
4
Ngakhale kuti nduna zake zafika kale ku Zowani, ndipo akazembe ake afika kale ku Hanesi,
5
anthu onse a ku Yuda adzamva manyazi chifukwa cha anthu opanda nawo phindu ndipo osaŵathandiza konse, koma ongobweretsa manyazi.”
6
Nawu ulosi wonena za nyama za ku chipululu chakumwera: Akazembe akuyenda m'dziko loopsa m'mene muli mikango, mphiri ndi njoka zouluka. Amasenzetsa abulu ao mphatso zamtengowapatali ndipo chuma chao amasenzetsa ngamira zao, kupita kwa mtundu wa anthu umene sungaŵathandize.
7
Chithandizo cha Ejipito nchachabe ndi chopanda phindu, choncho dzikolo ndalitcha dzina lakuti “Chilombo cholibwidika.”
8
Mulungu adandiwuza kuti, “Tsopano pita, ukalembe zimenezi pa sileti iwo akuwona, ukazilembenso m'buku, kuti kutsogolo zidzakhale umboni wosatha.
9
Ameneŵa ndi anthu opandukira Mulungu, ana onama, okana kumvera malangizo a Chauta.
10
Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’ Amauza aneneri kuti, ‘Musatiloserenso zoona. Mutiwuze zotikomera, mutilosere zam'mutu chabe.
11
Chokani apa, osakhala pa njira. Sitifuna kumvanso za Woyera uja wa Israele.’ ”
12
Nchifukwa chake Woyera uja wa Israele akunena kuti, “Inu mumanyozera zimene ndimakuuzani, mumakhulupirira zopsinja anzanu ndipo mumadalira mabodza.
13
Nchifukwa chake tchimo lanuli lidzakhala ngati mng'ankha pa chipupa chachitali choŵinuka, chimene kugwa kwake nkwadzidzidzi.
14
Zidzakhala ngati kuphwanyika kwa mbiya, imene ili yotekedzekeratu, popanda ndi phale lomwe lopalira moto, kapena lotungira madzi m'chitsime.”
15
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
16
Mudati, “Tidzathamanga pa akavalo.” Chabwino, mudzathaŵe! Mudatinso, “Tidzakwera pa magareta aliŵiro.” Chabwino, koma okuthamangitsani adzakhalanso aliŵiro.
17
Anthu chikwi chimodzi mwa inu adzathaŵa poona mdani mmodzi. Asilikali asanu okha adzakwanira kukuthamangitsani. Otsalira mwa inu adzakhala ngati mtengo wa mbendera wapaphiri, ngati chizindikiro chapagomo.
18
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
19
Ndithudi, inu anthu a ku Ziyoni, okhala ku Yerusalemu, simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu, ndipo akadzangomva, pompo adzakuyankhani.
20
Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona.
21
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
22
Pamenepo mudzatenga mafano anu, ena okutidwa ndi siliva, ena okutidwa ndi golide, ndipo mudzaŵataya ngati zinyalala, ndikunena kuti, “Zichoke zonsezi!”
23
Mukamadzabzala mbeu zanu, Chauta adzakugwetserani mvula kuti zimere, ndipo mudzakolola zambiri. Tsiku limenelo ng'ombe zanu zidzapeza mabusa aakulu.
24
Ng'ombe ndi abulu zokuthandizani kulima zidzadya chakudya chamchere chopapasa ndi fosholo ndi chifoloko.
25
Pa tsiku limene nsanja zankhondo za adani anu zidzagwe, anthu ake naphedwa, pa phiri lililonse lalikulu ndi pa gomo lililonse lalitali, padzayenda mitsinje ya madzi.
26
Mwezi udzaŵala ngati dzuŵa, ndipo dzuŵa lidzaŵala kwambiri ngati kasanunkaŵiri kuŵala kwa pa tsiku limodzi. Zimenezi zidzachitika pamene Chauta adzamange ndi kupoletsa zilonda zimene Iye yemwe adachititsa pakuŵalanga anthu ake.
27
Onani, ulemerero wa Chauta ukuwonekera kuchokera kutali. Akuwonetsa mkwiyo m'kati mwa moto ndi m'kati mwa chiwutsi chatolotolo. Akulankhula mwaukali, ndipo mau ake akutentha ngati moto woononga.
28
Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, wa madzi oyesa m'khosi. Akusefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza. Ngati akavalo, akuŵaika m'kamwa chitsulo choti chiŵasokeretse.
29
Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele.
30
Chauta adzamveketsa liwu lake loopsa, ndipo anthu adzaona dzanja lake likutsika pa iwo, ndi ukali woopsa ndi malaŵi a moto woononga, pakati pa mphezi, namondwe ndi matalala.
31
Aasiriya adzaopsedwa ndi liwu la Chauta, pamene Iye adzaŵakantha ndi ndodo yake.
32
Pamene Mulungu adzakhala akuŵalanga adani aja, anthu ake adzakhala akuvina ndi ting'oma ndi azeze. Mulungu mwini adzamenyana ndi Aasiriya.
33
Malo otenthera zinthu ndi okonza kale, adakonzera mfumu ya ku Asiriya. Malowo ndi ozama ndi aakulu, odzaza ndi moto ndi nkhuni. Tsono mpweya wa Chauta, wonga ngati mtsinje wa sulufure, udzakoleza motowo.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→