bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 65
Isaiah 65
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 64
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 66 →
1
Chauta adati, “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a anthu amene sadandipemphere. Ndinali wokonzeka kuti andipeze anthu amene sadandifunefune. Mtunduwo sudapemphere kwa Ine ngakhale nthaŵi zonse ndinali wokonzeka kuŵayankha kuti, ‘Ine ndili pano, ndikuthandizani.’
2
Nthaŵi zonse ndakhala wokonzeka kuŵalandira mwaufulu anthu ondipandukiraŵa, amene amachita zoipa namatsata njira zao chifukwa cha kuuma mitu kwao.
3
Amandikwiyitsa mopanda manyazi. Amapereka nsembe zachikunja m'minda, ndipo amafukiza lubani pa maguwa anjerwa achikunja.
4
Amakatandala ku manda, amachezera kumalo obisika usiku. Amadya nyama yankhumba, namamwa msuzi wa nyama zoperekera nsembe zachikunja.
5
“Amauza ena kuti, ‘Khalani panokha, osatiyandikira, chifukwa ndife opatulika.’ Sindingathe kupirira nawo anthu otere. Ukali wanga pa iwo uli ngati moto wosazima.
6
Ndatsimikiza kale za chilango chao, ndipo mlandu wao ndaulemba kale. Ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.
7
Ndidzaŵalanganso chifukwa cha machimo a makolo ao. Iwowo afukiza lubani pa mapiri a mafano achikunja, ndipo andinyoza Ine pa zitunda zao. Nchifukwa chake ndidzaŵalanga potsata zimene achita.”
8
Chauta akuti, “Pamene madzi adakalimo m'mphesa, anthu amati, ‘Musaziwononge, zokoma zidakalimo.’ Inenso ndidzaŵatero anthu anga, sindidzaŵaononga onse.
9
M'banja la Yakobe ndidzatulutsamo zidzukulu, ndipo a m'banja la Yuda adzalandira dziko langa lamapiri ngati choloŵa chao. Anthu anga osankhidwa adzalilandiradi, atumiki anga adzakhala kumeneko.
10
Chigwa cha Saroni chidzakhala busa la nkhosa, ndipo Chigwa cha Akori chidzasanduka malo ousirapo msambi wa ng'ombe, kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
11
Koma inu amene mumakana Chauta, amene mumaiŵala phiri langa lopatulika, amene mumapembedza Gadi ndi Meni, milungu yobweretsa mwai ndi tsoka,
12
nonsenu ndidzakufetsani ku nkhondo. Nonsenu mudzaphedwadi, chifukwa simudayankhe m'mene ndidakuitanani, ndipo simudamve m'mene ndidalankhula, koma mudachita zoipa pamaso panga. Mudasankha kuchita zoipa m'malo mwa zabwino.”
13
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu. Atumiki anga adzakondwa, koma inu mudzakhala ndi manyazi.
14
Iwo adzaimba mokondwa, koma inu mudzalira kwambiri chifukwa chovutika mu mtima. Mudzalira mofuula chifukwa cha kumva kuŵaŵa mu mtima.
15
Anthu anga osankhidwa adzatchula dzina lanu potemberera, ndipo Ine Chauta ndidzakuphani. Koma amene amandimvera ndidzaŵapatsa dzina lina latsopano.
16
Motero wopempha madalitso m'dzikomo, adzachita zimenezo kwa Mulungu wolankhula zoona. Ndipo wochita malumbiro m'dzikomo, adzalumbira m'dzina la Mulungu wolankhula zoona, chifukwa choti mavuto akale aiŵalika ndipo achotsedwa pamaso panga.”
17
Chauta akunena kuti, “Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zakale sadzazikumbukiranso, zidzaiŵalika kotheratu.
18
Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya, chifukwa cha zimene ndidzalenga. Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano wodzaza ndi chimwemwe, ndipo anthu ake adzakhala okondwa.
19
Mwiniwakene ndidzakhala wokondwa kwambiri chifukwa cha Yerusalemu, ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu ake. Kumeneko sikudzamvekanso kulira kapena kudandaula.
20
Ana sadzafanso ali akhanda, ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zao zonse. Amene adzafe ali a zaka zana limodzi zokha adzaoneka ngati anyamata. Kufa zisanakwane zaka zana limodzi kudzasonyeza kutembereredwa.
21
Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo. Adzabzala mipesa, ndipo adzadyerera zipatso zake.
22
Sadzamanga nyumbazo kuti anthu ena azikhalamo, ndipo sadzabzala mipesayo kuti anthu ena azidyerera zipatso zake. Anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo. Ndipo anthu anga osankhidwa adzakondwerera ntchito za manja ao nthaŵi yaitali.
23
Sadzagwira ntchito pachabe, kapena kubereka ana kuti aone tsoka, chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Chauta, iwowo ndi zidzukulu zao zomwe.
24
Ndidzaŵayankha asanatsirize nkomwe kupemphera, ndidzaŵamva akulankhula kumene.
25
Mimbulu ndi anaankhosa zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ng'ombe. Fumbi ndiye lidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa loyera la Ziyoni sipadzakhala chinthu chopweteka kapena choononga,” akuterotu Chauta.
← Chapter 64
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 66 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→