bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 9
Isaiah 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 10 →
1
Koma anthu amene anali ndi nkhaŵa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina.
2
Anthu amene ankayenda mumdima aona kuŵala kwakukulu. Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani, kuŵala kwaŵaonekera.
3
Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m'mene anthu amakondwera nthaŵi ya masika, monganso m'mene anthu amakondwera pogaŵana zofunkha.
4
Pakuti inu mwathyola goli limene linkaŵalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu oŵazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani.
5
Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi, zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni.
6
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
7
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.
8
Ambuye atumiza mau otsutsa Yakobe, mauwo agwa pa Aisraele, zidzukulu zake.
9
Anthu onse, ndiye kuti Aefuremu ndi anthu okhala m'Samariya, adzazimva zotsatira zake za mau ameneŵa. Iwo amalankhula monyada ndi modzikuza kuti,
10
“Ngakhale njerwa zagumuka, ife tidzamanga ndi miyala yosema. Ngakhale mitanda yamkuyu yagwetsedwa, ife tidzaika mitanda yamkungudza m'malo mwake.”
11
Koma Chauta waŵautsira adani, Waŵakhwirizira adaniwo kuti amenyane nawo.
12
Asiriya chakuvuma ndi Afilisti chakuzambwe ayasama kukamwa kuti adye Aisraele. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
13
Anthuwo sadabwerere kwa Mulungu amene adaŵakantha uja, sadalape ndi kufunafuna Chauta Wamphamvuzonse.
14
Nchifukwa chake Chauta wadula mutu wa Israele pamodzi ndi mchira womwe, nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe pa tsiku limodzi.
15
Mutuwo ukutanthauza akuluakulu ndi olemekezeka, mchirawo ukutanthauza aneneri ophunzitsa zabodza.
16
Pakuti amene amatsogolera anthuŵa amaŵasokeza, ndipo otsogoleredwawo amatayika.
17
Nchifukwa chake Ambuye sadzakondwera nawo achinyamata, ndipo sadzaŵachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye. Pakuti aliyense ndi wosasamala za Mulungu ndiponso ndi wochimwa. Pakamwa paliponse pamalankhula zopusa. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
18
Kuipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto, moto wake wotentha mkandankhuku ndi minga. Umayatsanso nkhalango ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo wochindikira.
19
Nchifukwa chake mkwiyo wa Chauta Wamphamvuzonse watentha dziko, ndipo anthu ali ngati nkhuni zosonkhera moto. Palibe munthu wochitira chifundo mbale wake.
20
Ku dzanja lamanja amapeza ndi kudya chakudya, koma osakhuta, ku dzanja lamanzere amapeza ndi kudya chakudya, koma njala ali nayobe. Kwatsala nkumangodyana okhaokha.
21
Amanase akuthira Aefuremu nkhondo, Aefuremu akuthira Amanase nkhondo. Onsewo pamodzi akumenyana ndi Yuda. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→