bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 5
Isaiah 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 6 →
1
Ntamuimbirako bwenzi langa nyimbo yokamba za wokondedwa wanga ndi munda wake wamphesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde.
2
Adautipula nachotsa miyala yonse, ndipo adaokamo mipesa yabwino kwabasi. Adamanga nsanja pakati pa mundawo, nasema mopondera mphesa m'kati momwemo. Adaayembekeza kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ai, udabala mphesa zachabechabe.
3
Ndiye wokondedwa wanga akuti, “Inu amene mumakhala ku Yerusalemu, ndi inu anthu a ku Yuda, ndakupembani, taweruzani pakati pa ine ndi munda wanga wamphesawu.
4
Kodi chilipo chinanso chimene ndidaayenera kuuchitira munda wanga wamphesa, koma sindidachite? Pamene ndinkayembekeza kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji udabala mphesa zachabechabe?
5
“Tsopano taimani nkuuzeni zimene ndidzauchite munda wanga wamphesawo. Ndidzazula mpanda wake, ndipo mundawo udzaonongeka. Ndidzagwetsa chipupa chake, ndipo nyama zidzapondapondamo.
6
Ndidzausandutsa tsala, udzakhala wosatengulira ndi wosalimira, ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina. Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pamundapo.”
7
Tsonotu munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonseyo ndi dziko la Israele, ndipo Ayuda ndiwo mipesa yake yokondweretsa. Iye ankayembekeza ntchito zabwino, koma adangoona kuphana. Ankayembekeza chilungamo, koma adangomva kulira kwa anthu ozunzidwa.
8
Tsoka kwa amene amangokhalira kulumikiza nyumba amene amangokhalira kuwonjezera minda, mpaka kulanda malo onse, kuti dziko lonse likhale la iwo okha.
9
Ndamva Chauta Wamphamvuzonse akulumbira kuti: “Ndithudi, nyumba zambirizo zidzasanduka mainja, nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
10
Munda wamphesa wa mahekitara khumi, vinyo wake adzangodzaza mbiya imodzi. Kufesa madengu khumi a mbeu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”
11
Tsoka kwa amene amadzuka m'mamaŵa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu.
12
Amangoimba zeze, pangwe, ng'oma ndi chitoliro, nkumamwa vinyo pa maphwando ao. Koma sasamala ntchito za Chauta, sapenya ntchito za manja ake.
13
Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo chifukwa cha kusamvetsa zinthu. Atsogoleri ao olemekezeka adzafa ndi njala, ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
14
Nchifukwa chake kumanda sikukhuta, kwangoti kukamwa yasa kuti kulandire aliyense. Anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka, adzagweramo ali wowowo, m'kuledzera kwaoko.
15
Munthu aliyense adzatsitsidwa, onse adzachepetsedwa, anthu odzikuza adzaŵachititsa manyazi.
16
Koma Chauta Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chake, Mulungu Woyera adzaonetsa kuyera kwake pochita zaungwiro.
17
Tsono anaankhosa adzadya pamenepo ngati pabusa pao, ndipo anaambuzi adzadya m'mabwinja.
18
Tsoka kwa amene amadzikokera machimo ambiri ndi kunama kwao, amene amalephera kudzimasula ku machimo awo.
19
Amanena kuti, “Chauta afulumire, agwire ntchito yake mwamsanga, kuti ntchitoyo tiiwone. Zimene Woyera uja wa Israele afuna kuchita, zichitiketu kuti tizidziŵe.”
20
Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa!
21
Tsoka kwa amene amadziwona ngati anzeru ndipo amadziyesa ochenjera!
22
Tsoka kwa zidakwa zimene zimaika mtima pa vinyo! Tsoka kwa anthu amene saopa konse kusakaniza zakumwa zaukali!
23
Amalungamitsa wolakwa chifukwa cha chiphuphu nkuipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24
Nchifukwa chake monga momwe moto umaonongera chiputu, monga momwenso udzu wouma umapsera m'malaŵi a moto, momwemonso muzu wao udzaola, ndipo maluŵa ao adzafota ndi kuuluka ngati fumbi, chifukwa adakana malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, adanyoza mau a Woyera uja wa Israele.
25
Nchifukwa chake ukali wa Chauta waŵayakira anthu ake. Iye watambalitsa dzanja lake pa anthuwo kuti aŵakanthe. Mapiri agwedezeka, ndipo mitembo ya anthuwo yangoti mbwee ngati zinyalala pakati pa miseu. Koma ngakhale Mulungu watero, mkwiyo wake sudaleke, dzanja lake lidakali chitambalitsire.
26
Chauta adzapereka chizindikiro kuitana mtundu wa anthu akutali. Adzaŵaitana anthuwo ndi khweru, kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Tsono iwo adzabweradi mothamanga kwambiri.
27
Palibe ndi mmodzi yemwe wodzatopa kapena kukhumudwa, kuwodzera kapena kugona. Palibe lamba wam'chiwuno amene adzamasuke, palibe chingwe cha nsapato zao chimene chidzaduke.
28
Mivi yao ndi yakuthwa, mauta ao onse ngokoka, ziboda za akavalo ao nzolimba ngati mwala, magaleta ao ndi aliŵiro ngati kamvulumvulu.
29
Kufuula kwao kuli ngati kubangula kwa mkango, amabangula ngati misona ya mkango, imene imadzuma pogwira nyama, nipita nazo popanda ndi mmodzi yemwe wozipulumutsa.
30
Tsiku limenelo adzaŵakokolola monga momwe mtsinje waukulu umakokololera chilichonse chomwe chili mu njira yake ndi mkokomo wa madzi amphamvu. Ndipo wina kuti ayang'ane dzikolo, adzangoona mdima ndi zovuta. Ngakhale kuŵala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66