bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 44
Isaiah 44
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 45 →
1
Chauta akunena kuti, “Mverani tsopano, inu am'banja la Yakobe. Inu Aisraele, ndinu atumiki anga, osankhidwa anga.
2
Ine ndine Chauta amene ndidakulengani ndi kukuumbani m'mimba mwa amai anu, amenenso ndinkakuthandizani. Usaope iwe Yakobe, mtumiki wanga. Inu ndinu anthu anga okondedwa amene ndidakusankhulani.
3
Ndidzathira madzi pa dziko louma, ndidzayendetsa mitsinje m'chipululu. Ndidzatumizira ana anu Mzimu wanga, ndidzatsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
4
Iwo adzakula bwino ngati udzu wothirira bwino, ngati misondodzi yomera m'mbali mwa mitsinje.
5
Wina adzanena kuti ‘Ine ndine wa Chauta,’ wina adzadzitchula wa m'banja la Yakobe. Winanso adzalemba padzanja pake kuti, ‘Wa Chauta,’ ndipo adzadzitchula wa m'banja la Israele.”
6
Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele, Chauta Mphambe, akunena kuti, “Ine ndine woyamba ndi womaliza. Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha.
7
Ndani nanga akulingana ndi Ine? Aimirire, alankhule, andifotokozere. Kuyambira kalekale ndani adalosa zakutsogolo? Atidziŵitsetu zimene zikudzachitika.
8
Musadedere, musaope. Suja kuyambira kale lomwe ndakhala ndikukuuzani ndi kutsimikiza zimenezi? Inuyo ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine? Iyai, palibenso Thanthwe lina, sindikudziŵa lina lililonse.”
9
Onse amene amapanga mafano ngachabe, milungu imene amailemekeza kwambiri ndi yopanda phindu. Amene amaipembedza ndi akhungu ndi osadziŵa kanthu, choncho adzaŵachititsa manyazi.
10
Phindu lake nchiyani kupanga kamulungu kapena kusungunula fano lachabechabe?
11
Onse opembedza fanolo adzaŵachititsa manyazi. Opanga mafano ndi anthu chabe. Onse asonkhane, aonekere ku bwalo la milandu. Onsewo adzaopsedwa, ndipo adzachita manyazi.
12
Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo nachiika pa moto. Ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pakuchimenya ndi nyundo. Pambuyo pake amamva njala natha mphamvu, akapanda kumwa madzi, amalefuka.
13
Mmisiri wa matabwa amayesa mtengo ndi chingwe. Amalembapo chithunzi ndi cholembera, nachizokota ndi zipangizo zake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola, kuti achiike m'nyumba ya chipembedzo.
14
Amagwetsa mitengo ya mkungudza. Mwinanso amasankhula mtengo wa paini kapena wa thundu ku nkhalango. Mwina mwake amabzala mtundu wina wa paini ndipo umakula ndi mvula.
15
Mtengowo munthu amachitako nkhuni. Nthambi zina amasonkhera moto wootha, zina moto wophikapo buledi. Chigawo china cha mtengowo amapangira kamulungu nayamba kukapembedza. Amapanga fano namaligwadira.
16
Chigawo china amasonkhera moto wootchapo nyama imene amadya mpaka kukhuta. Amaothanso motowo namanena kuti, “Aha! Ndikumva kufunda! Ati kukoma motowu ati!”
17
Ndi chigawo chotsala amapanga kamulungu kake, fano lake limenelo. Amaliŵeramira ndi kumalipembedza. Amapemphera kwa fanolo namanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, undipulumutse.”
18
Anthu otere sadziŵa kanthu ndipo samvetsa konse. Maso ao ndi omatirira, sangathe kupenya. Nzeru zaonso nzogontha, sangathe kumvetsa.
19
Palibe wolingalira, palibe wanzeru kapena womvetsa woti anganene kuti, “Chigawo china cha mtengo ndidatentha pa moto, pa makala ake ndidaphikapo buledi, ndidaotchapo nyama ndipo ndidadya. Tsopano chigawo chotsalachi ndipangira chinthu chonyansa! Monga ine ndizipembedza mtengo?”
20
Munthuyo akuchita ngati kudya phulusa, maganizo ake opusa amsokeretsa kotero kuti sangapulumutsenso moyo wake. Sangathenso kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili m'manja mwangachi si chabodza?”
21
Chauta akunena kuti, “Ukumbukire zimenezi, iwe Yakobe, popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israele. Ndidakulenga, ndiwe mtumiki wanga. Iwe Israele sindidzakuiwala.
22
Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”
23
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga, pakuti Chauta wagwiradi ntchito. Fuula iwe dziko lapansi. Yambani nyimbo, inu mapiri, ndiponso inu nkhalango ndi mitengo yanu yonse, chifukwa Chauta waombola Yakobe, waonetsa ulemerero wake mwa Israele.
24
Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza?
25
Ndine amene ndimalepheretsa mipingu ya anthu onama, ndi kupusitsa anthu oombeza ula. Ndine amene ndimatsutsa mau a anthu anzeru, ndi kuŵaonetsa kuti nzeru zao nzopusa.
26
Ndine amene ndimatsimikiza mau a mtumiki wanga, ndi kupherezetsa zimene amithenga anga adaneneratu. Ndine amene ndimanena za Yerusalemu kuti anthu adzakhalanso kumeneko, ndi kunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti idzamangidwanso. Ine ndidzautsanso malo ao amene adagwetsedwa.
27
Ndine amene ndimauza nyanja yaikulu kuti, ‘Uma, ndipo mitsinje yakonso ndiiwumitsa.’
28
Ndine amene ndimanena za Kirusi kuti ‘Iye uja ndi mbusa wanga, adzachita zonse zimene ndikulinga! Adzalamula kuti Yerusalemu amangidwenso, ndipo kuti maziko a Nyumba ya Mulungu aikidwe.’ ”
← Chapter 43
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 45 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→