bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 40
Isaiah 40
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 41 →
1
“Atonthozeni mtima, atonthozeni mtima anthu anga,” akutero Mulungu wanu.
2
“Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.”
3
Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu.
4
Chigwa chilichonse achidzaze, phiri lililonse ndi gomo lililonse alitsitse. Dziko lokumbikakumbika alisalaze, malo azitundazitunda aŵasandutse zidikha.
5
Motero ulemerero wa Chauta udzaoneka, anthu onse adzauwona. Chauta mwini wake ndiye wanena zimenezi.”
6
Kudamveka mau akuti, “Lengeza.” Ine ndidafunsa kuti, “Kodi ndilengeze chiyani?” Mau aja adati, “Ulengeze kuti anthu onse ali ngati udzu. Kukongola kwao kuli ngati maluŵa akuthengo.
7
Udzu umauma, maluŵa amafota, Chauta akaziwuzira mpweya wake. Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
8
Udzu umauma, maluŵa amafota, koma mau a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
9
Kwera pa phiri lalitali, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Yerusalemu. Ufuule kwamphamvu, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Ziyoni. Kweza mau, usaope. Uuze mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera.”
10
Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake.
11
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
12
Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo?
13
Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta? Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake?
14
Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?
15
Mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko, ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo. M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi.
16
Nkhalango ya ku Lebanoni siingakwanitse nkhuni zosonkhera moto, nyama zam'menemo sizingakwanire kuperekera nsembe yootcha.
17
Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake.
18
Kodi Mulungu mungathe kumuyerekeza ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
19
Likakhala fano, ndi munthu waluso amene amalipanga, kenaka mmisiri wa golide amalikuta ndi golide, nalipangira ukufu wasiliva.
20
Mmphaŵi wosatha kupeza choperekera nsembe, amasankhula mtengo umene sudzaola. Amafunafuna mmisiri woti ampangire fano limene silingagwedezeke.
21
Monga simudadziŵe? Monga simudamve? Kodi poyamba ponse sadakuuzeni? Kodi simudamvetse za kakhazikitsidwe ka dziko lapansi?
22
Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu.
23
Amatsitsa mafumu amphamvu, olamulira dziko amaŵasandutsa achabechabe.
24
Iwo ali ngati mbeu zobzala posachedwa, kapena zofesa chatsopano, zongoyamba kumene kuzika mizu. Mbeuzo Chauta akaombetsa mphepo zimauma, ndipo mkuntho umaziwulutsa ngati mankhusu.
25
Woyera Uja akuti, “Kodi mungathe kundiyerekeza ndi yani? Kodi alipo wina wolingana nane?”
26
Yang'anani kumlengalenga. Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi? Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo, ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake. Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu. Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo.
27
Iwe Yakobe, ukulankhuliranji? Iwe, Israele, ukuneneranji kuti Chauta sakudziŵa za mavuto ako, kapenanso kuti sakusamalapo za iwe?
28
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
29
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.
30
Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa.
31
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 41 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→