bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 3
Isaiah 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 4 →
1
Tsopano Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, ali pafupi kulanda Yerusalemu ndi Yuda chithandizo cha mtundu uliwonse chimene anthu amadalira. Adzachotsa chakudya chonse, adzachotsa madzi onse,
2
anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo, aweruzi ndi aneneri, olosa ndi akuluakulu,
3
atsogoleri ankhondo ndi anthu olemekezeka, aphungu ndi amatsenga, ndiponso akatswiri a njirisi.
4
Adzaŵaikira anyamata kuti akhale mafumu ao, ndipo ana amakanda ndiwo adzaŵalamulira.
5
Anthu adzazunzana, aliyense adzazunza mnzake. Anyamata adzachita chipongwe akuluakulu, ndipo anthu achabechabe adzanyoza olemekezeka.
6
Munthu adzagwira mbale wake m'nyumba ya atate ao, nkunena kuti, “Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu nthaŵi yamavutoyi.”
7
Tsiku limenelo mbale wakeyo adzayankha kuti, “Ine ai toto! Mavuto otereŵa ndilibe mankhwala ake, m'nyumba mwanga momwe ndilibe chakudya kapena chovala. Musaike ine kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu.”
8
Zoonadi Yerusalemu akusakazika ndipo Yuda akugwa, chifukwa zokamba ndiponso ntchito za anthu am'menemo nzonyoza Chauta. Salabadako za ulemerero wa Mulungu.
9
Maonekedwe a nkhope zao amaŵatsutsa. Amachimwa poyera ngati m'mene ankachitira anthu a mu Sodomu, sabisa konse. Tsoka kwa iwowo, achita kudziputira okha mavuto.
10
Ngodala anthu omvera Mulungu pakuti zinthu zidzaŵayendera bwino, adzakondwera ndi phindu la ntchito zao.
11
Koma tsoka kwa anthu oipa! Zinthu zidzaŵaipira. Zimene akhala akuchitira anzao zomwezo zidzaŵabwerera.
12
Inu anthu anga, amene akukuponderezani ndi ana chabe, ndipo amene akukulamulani ndi akazi. Aah! Anthu anga, atsogoleri anu akukusokeretsani, akukusokonezerani njira zanu.
13
Tsopano Chauta afuna kuyambapo mlandu, wakonzeka kale kuweruza anthu ake.
14
Chauta akuŵaimba mlandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake. Akuŵazenga kuti, “Ndinu amene mwaononga munda wanga wamphesa. Nyumba zanu zadzaza ndi zinthu zolanda kwa amphaŵi.
15
Mukuŵapsinjiranji anthu anga? Chifukwa chiyani mukuŵadyera masuku pamutu amphaŵi?” Akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
16
Chauta adati, “Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri: amayenda makosi ali wee, amayang'ana ndi maso ophika. Amayenda nyang'anyang'a ndi kuliza zigwinjiri zam'miyendo.
17
Nchifukwa chake Ambuye adzatulutsa zipere kumutu kwa akazi a ku Ziyoniwo, tsitsi lao lonse lidzatha phu!”
18
Tsiku limenelo Ambuye adzaŵachotsera zokongoletsera m'miyendo, kumutu ndi m'khosi,
19
maukufu, makoza, ndi nsalu zakumaso,
20
maduku, zigwinjiri, malamba, mabotolo a zonunkhira, zithumwa,
21
mphete, zipini,
22
madelesi apaphwando, makepi, miinjiro, zikwama,
23
akalilole, zovala zabafuta, nduŵira, ndiponso nsalu zam'mapewa.
24
M'malo mwa kununkhira padzakhala kununkha, m'malo mwa lamba adzavala chingwe, m'malo mwa tsitsi lopesa bwino adzakhala ndi mipala, m'malo mwa delesi la mtengo wapatali adzavala chiguduli, m'malo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
25
Iwe Yerusalemu, anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu ako amphamvu adzafera ku nkhondo.
26
Choncho pa zipata zako padzakhala kulira kokhakokha, iweyo udzasakazidwa nkukhala pansi, ukuvimvinizika pa fumbi.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66