bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 13
Isaiah 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 14 →
1
Nawu uthenga wonena za Babiloni umene Yesaya, mwana wa Amozi, adalandira kwa Mulungu.
2
Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see. Muŵafuulire ankhondo ndi kuŵakodola kuti adzaloŵe pa zipata za mzinda.
3
Ine Mulungu mwini wake ndapereka malamulo kwa anthu anga opatulika. Ndasonkhanitsa ankhondo amphamvu, amene amakondwerera kupambana kwanga, kuti akhale zida zanga zolangira amene ndimaŵakwiyira.
4
Tamvani phokoso kumapiriku! Likumveka ngati phokoso la chinamtindi cha anthu. Imvani chiwawa m'maufumu! Ndiye ngati mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi. Chauta Wamphamvuzonse akukhazika ankhondo ake mokonzekera kumenya nkhondo.
5
Iwowo akuchokera ku maiko akutali, ku malekezero a dziko. Ndiye kuti Chauta wanyamula zida zake zija mokwiya, akubwera kuti adzaononge dziko lonse lapansi.
6
Lirani kwamphamvu pakuti tsiku la Chauta layandikira. Likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe.
7
Tsono manja onse adzafooka, ndipo mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
8
Onse adzada nkhaŵa, adzavutika ndi kumva zoŵaŵa, zoŵaŵa zake zonga zimene amazimva mkazi pochira. Azidzayang'anana mwamantha, nkhope zao zidzagwa ndi manyazi.
9
Zoonadi, tsiku la Chauta likudza, tsiku lopanda chisoni, laukali ndi lamkwiyo. Chauta akubwera kuti asandutse dziko lapansi chipululu ndi kuwononga anthu ochimwa am'menemo.
10
Nyenyezi zonse zakumwamba sizidzaonetsanso kuŵala. Dzuŵa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzaŵala konse.
11
Chauta akuti, “Ndidzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha kuipa kwao, ndidzalanga oipa chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
12
Anthu ndidzaŵasandutsa osapezekapezeka kuposanso m'mene aliri golide wangwiro, mtundu wa anthu udzakhala wosoŵa ngati golide wa ku Ofiri.
13
Tsono ndidzagwedeza mlengalenga, ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Ine Chauta Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wanga woopsa.
14
Choncho munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwao, aliyense adzathaŵira ku dziko lake, ngati mbaŵala zothaŵa anthu auzimba kapenanso ngati nkhosa zopanda wozikusa.
15
Aliyense amene adzapezeke adzabayidwa chipyoza. Aliyense amene adzagwidwe adzaphedwa ndi lupanga.
16
Ana ao akhanda adzatswanyidwa iwo akuwona. M'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndipo akazi ao adzaŵachimwitsa mwakhakhamizo.
17
“Ine Chauta ndidzadzutsa Amedi kuti amenyane ndi Ababiloni. Iwo safuna siliva ndipo sakondwa ndi golide.
18
Adzapha anyamata ndi mauta ao. Sadzachitira chifundo ana. Mitima yao siidzamva chisoni ndi ana akhanda omwe.
19
Babiloni ufumu wake ndi waulemerero kuposa maufumu ena onse, ndipo anthu ake amaunyadira. Koma Ine Chauta ndidzaononga mzinda wa Babiloniwo monga ndidaonongera Sodomu ndi Gomora pa nthaŵi imene ndidagonjetsa mizindayo.
20
Anthu sadzakhalamonso kapena kukhazikikamo pa mibadwo yonse. Mluya aliyense woyendayenda sadzamangako hema kumeneko, abusa sadzaŵetako ziŵeto zao kumeneko.
21
Koma nyama zakuthengo ndizo zimene zidzakhale kumeneko, nyumba zake zidzadzaza ndi akadzidzi. Kuzidzayendayenda nthiŵatiŵa, ndipo atonde akuthengo azidzavinavinako.
22
M'nsanja zake muzidzalira afisi, m'nyumba zake zaufumu zokongola muzidzalira nkhandwe. Nthaŵi yake yayandikira, ndithu masiku ake ali pafupi kutha.”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→