bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 16
Isaiah 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 17 →
1
Amowabu atumiza mphatso ya mwanawankhosa kwa wolamulira dziko. Iwo achokera ku mzinda wa Sela, adzera njira ya chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
2
Monga momwe mbalame zimaulukira uku ndi uku akazimwaza m'chisa, momwemonso akazi a ku Mowabu akuyendayenda ku madooko a Arinoni.
3
Akuuza anthu a ku Yuda kuti, “Mutiwuze chochita, gamulani zoti tichite. Pamene dzuŵa lili pa liwombo, mutipatse mthunzi wabii ngati mdima. Mutibise ife anthu opirikitsidwa, musatipereke ife anthu othaŵa nkhondo.
4
Othaŵa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu. Mukhale populumukira pao kwa woononga uja.” Nthaŵi ikudza pamene kupsinja sikudzakhalaponso, kuwononga kudzaleka, ndipo amene amaŵapondereza adzachoka m'dzikomo.
5
Pamenepo mpando wachifumu udzakhazikitsidwa mwachikondi, mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata zachilungamo, ndipo adzalimbikira kuchita zaungwiro.
6
Anthu a ku Yuda akunena kuti, “Kudzikuza kwa Amowabu takumva, adadzikuza kwambiri. Kudzitukumula kwao, kunyada kwao, kunyodola kwao ndi kudzitama kwao, zonse nzachabechabe.”
7
Nchifukwa chake alekeni Amowabu alire kwambiri, onsewo alire fuko lao, Alire motaya mtima chifukwa cha makeke amphesa amene ankadya ku Kiri-Haresefi.
8
Paja minda ya ku Hesiboni idaguga, yatha pamodzi ndi minda yamphesa ya ku Sibima. Mphesa zake zinkaledzeretsa olamulira anthu a mitundu ina. Kale nthambi zake zinkafika mpaka ku Yazere ndi ku chipululu, ndiponso mpaka kutsidya kwa nyanja.
9
Nchifukwa chake ndikulira monga m'mene akulirira anthu a mu mzinda wa Yezere chifukwa cha minda yamphesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni ndi Eleale ndikukunyowetsani misozi chifukwa choti mwalephera kupeza zokolola, kaamba ka nkhondo imene yaononga zonse.
10
Kukondwa ndi kusangalala kwalekeka ku minda yadzinthu. Nyimbo sizikuimbidwa, palibenso kufuula m'minda yamphesa. Palibe wopsinya vinyo mopondera mphesa, kufuula kwachimwemwe kwa nthaŵi yotchera mphesa kwalekeka.
11
Nchifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe, kulira Mowabu, mtima wanga ukubuula chifukwa cha kuwonongeka kwa Kiriheresi.
12
Ngakhale Amowabu akudzipereka pakupita ku akachisi ao namakapemphera mpaka kutopa, zimenezo sizidzaŵapindulira kanthu.
13
Mau ameneŵa ndiwo amene adalankhula Chauta kalekale kunena za Mowabu.
14
Koma tsopano akunena kuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata m'mene amaŵerengera munthu waganyu, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu. Chigulu chachikulu cha anthu ake chidzaonongeka, ndipo opulumukapo adzakhala ochepa ndi ofooka.”
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→