bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 10
Job 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 11 →
1
Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.
2
Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse; mundidziwitse chifukwa cha kutsutsana nane.
3
Chikukomerani kodi kungosautsa, kuti mupeputsa ntchito yolemetsa manja anu, ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?
4
Muli nao maso a thupi kodi? Mupenya kodi monga umo apenyera munthu?
5
Masiku anu akunga masiku a munthu kodi, zaka zanu zikunga masiku a munthu;
6
kuti mufunsa mphulupulu yanga, ndi kulondola choipa changa;
7
chinkana mudziwa kuti sindili woipa, ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?
8
Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu, koma mufuna kundiononga.
9
Mukumbukire kuti mwandiumba ngati dothi; ndipo kodi mudzandibwezera kufumbi?
10
Simunanditsanula kodi ngati mkaka, ndi kundilimbitsa ngati mase?
11
Munandiveka khungu ndi mnofu, ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha.
12
Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima, ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga.
13
Koma izi munazibisa mumtima mwanu; ndidziwa kuti ichi muli nacho.
14
Ndikachimwa mundipenya; ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga.
15
Ndikakhala woipa, tsoka ine; ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutu wanga; ndadzazidwa ndi manyazi, koma penyani kuzunzika kwanga.
16
Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango; mubweranso ndi kudzionetsera modabwitsa kwa ine.
17
Mundikonzeranso mboni zonditsutsa, ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu; nkhondo yobwerezabwereza yandigwera.
18
Potero munandibadwitsa chifukwa ninji? Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso.
19
Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala; akadanditenga pobadwapo kunka nane kumanda.
20
Masiku anga satsala owerengeka nanga? Lindani. Bandilekani kuti nditsitsimuke pang'ono,
21
ndisanachoke kunka kumene sindikabweranso, ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa.
22
Dziko la mdima bii ngati mdima wandiweyani, dziko la mthunzi wa imfa losalongosoka, kumene kuunika kukunga mdima.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42