bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 24
Job 24
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 25 →
1
Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo? Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?
2
Alipo akusendeza malire; alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.
3
Akankhizira kwao bulu wa amasiye, atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale chikole.
4
Apatukitsa aumphawi m'njira; osauka a padziko abisala pamodzi.
5
Taonani, ngati mbidzi za m'chipululu atulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya; chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao.
6
Atema dzinthu zao m'munda; natola khunkha m'munda wampesa wa woipa.
7
Agona amaliseche usiku wonse opanda chovala, alibe chofunda pachisanu.
8
Avumbwa ndi mvula kumapiri, nafukata thanthwe posowa pousapo.
9
Akwatula wamasiye kubere, natenga chikole chovala cha osauka;
10
momwemo ayenda amaliseche opanda chovala, nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.
11
M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta; aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.
12
M'mudzi waukulu anthu abuula alinkufa; ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula; koma Mulungu sasamalira choipacho.
13
Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika, sadziwa njira zake, Sasunga mayendedwe ake.
14
Kukacha auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi; ndi usiku asanduka mbala.
15
Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira, ndi kuti, Palibe diso lidzandiona; navala chophimba pankhope pake.
16
Kuli mdima aboola nyumba, usana adzitsekera, osadziwa kuunika.
17
Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa; pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.
18
Atengedwa ngati choyandama pamadzi; gawo lao litembereredwa padziko; sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa.
19
Chilala ndi dzuwa zitha madzi a chipale chofewa, momwemo manda achita nao ochimwa.
20
M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera. Sadzamkumbukiranso; ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo.
21
Alusira chumba wosabala, osamchitira wamasiye chokoma.
22
Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yake; iwo aukanso m'mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo.
23
Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo; koma maso ake ali pa njira zao.
24
Akwezeka; m'kamphindi kuli zii; inde atsitsidwa, achotsedwa monga onse ena, adulidwa ngati tirigu ngala zake.
25
Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza, ndi kuyesa mau anga opanda pake?
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42