bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 34
Job 34
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 35 →
1
Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,
2
Tamverani mau anga, inu anzeru; munditcherere khutu inu akudziwa.
3
Pakuti khutu liyesa mau, monga m'kamwa mulawa chakudya.
4
Tidzisankhire choyeneracho, tidziwe mwa tokha chokomacho.
5
Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama, ndipo Mulungu wandichotsera choyenera ine
6
Kodi ndidzinamizire? Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwa.
7
Wakunga Yobu ndani, wakumwa mwano ngati madzi?
8
Wakutsagana nao ochita mphulupulu, nayendayenda nao anthu oipa.
9
Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako kuvomerezana naye Mulungu.
10
Chifukwa chake mundimvere ine, eni nzeru inu, nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.
11
Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake, napezetsa munthu aliyense monga mwa mayendedwe ake.
12
Ndithu zoonadi, Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.
13
Anamuikiza dziko lapansi ndani? Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?
14
Akadzikumbukira yekha mumtima mwake, akadzisonkhanitsira yekha mzimu wake ndi mpweya wake,
15
zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi, ndi munthu adzabwerera kufumbi.
16
Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ichi, Tcherera khutu kunena kwanga.
17
Kodi munthu woipidwa nacho chiweruzo adzalamulira? Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?
18
Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pake iwe, kapena kwa akalonga, Oipa inu?
19
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
20
M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku, anthu agwedezeka, napita, amphamvu achotsedwa opanda dzanja lakuwachotsa.
21
Pakuti maso ake ali pa njira ya munthu aliyense, napenya moponda mwake monse.
22
Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa, kuti ochita zopanda pake abisaleko.
23
Pakuti Mulungu alibe chifukwa cha kulingiriranso za munthu, kuti afike kwa Iye kudzaweruzidwa.
24
Aphwanya eni mphamvu osatulutsa kubwalo mlandu wao, naika ena m'malo mwao.
25
Pakuti asamalira ntchito zao, nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.
26
Awakantha ngati oipa, poyera pamaso pa anthu,
27
popeza anapatuka, naleka kumtsata, osasamalira njira zake zilizonse.
28
M'mwemo anafikitsa kwa Iye kufuula kwa osauka; ndipo anamva Iye kufuula kwa ozunzika.
29
Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;
30
kuti munthu wonyoza Mulungu asachite ufumu, ndi anthu asakodwe mumsampha.
31
Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu, ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwa?
32
Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu, ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.
33
Kodi chilango cha Mulungu chikhale monga muchifuna inu, pakuti muchikana? Musankhe ndi inu, ine ai; m'mwemo monga mudziwa, nenani.
34
Anthu ozindikira adzanena nane, inde anthu anzeru onse akundimva adzati,
35
Yobu alankhula wopanda kudziwa, ndi mau ake alibe nzeru.
36
Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha, chifukwa cha kuyankha kwake monga anthu amphulupulu.
37
Pakuti pa kuchimwa kwake aonjeza kupikisana ndi Mulungu, asansa manja pakati pa ife, nachulukitsa maneno ake pa Mulungu.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42