bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 6
Job 6
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 7 →
1
Koma Yobu anayankha, nati,
2
Mwenzi atayesa bwino chisoni changa, ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso!
3
Pakuti zikadalemera tsopano koposa mchenga wa kunyanja; chifukwa chake mau anga ndasonthokera kunena.
4
Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
5
Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu? Ilira kodi ng'ombe pa chakudya chake?
6
Kodi chinthu chosakolera chidyeka chopanda mchere? Choyera cha dzira chikolera kodi?
7
Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza zikunga chakudya chosakolera kwa ine.
8
Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha, Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira!
9
Chimkomere Mulungu kundiphwanya, alole dzanja lake lindilikhe!
10
Pamenepo ndidzasangalala, ndidzakondwera nacho chowawa chosandileka; pakuti sindinawabisa mau a Woyerayo.
11
Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze? Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?
12
Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala? Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?
13
Mulibe thandizo mwa ine ndekha; chipulumutso chandithawa.
14
Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo; angaleke kuopa Wamphamvuyonse.
15
Abale anga anachita monyenga ngati kamtsinje, ngati madzi a timitsinje akupitirira.
16
Amada chifukwa cha madzi oundana. M'menemo chipale chofewa chibisika;
17
atafikira mafundi, mitsinje iuma; kukatentha, imwerera m'malo mwao.
18
Aulendo akutsata njira yao apatukapo, akwerera poti see, natayika.
19
Aulendo a ku Tema anapenyerera, makamu a ku Sheba anaiyembekezera.
20
Anazimidwa popeza adaikhulupirira; anafikako, nathedwa nzeru.
21
Pakuti tsopano mukhala momwemo; muona choopsa, muchitapo mantha.
22
Ngati ndinati, Mundipatse? Kapena, Muperekeko kwa ine chuma chanu?
23
Kapena, Mundilanditse m'dzanja la mdani? Kapena, Mundiombole m'dzanja la oopsa?
24
Mundilangize, ndipo ndidzakhala chete ine; mundizindikiritse umo ndinalakwira.
25
Mau oongoka si ndiwo amphamvu? Koma kudzudzula kwanu mudzudzula chiyani?
26
Kodi muyesa kudzudzula mau? Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.
27
Indetu, mugwetsera wamasiye msampha, mumkumbira bwenzi lanu mbuna.
28
Koma tsopano balindani, mundipenyerere; ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira.
29
Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu; inde, bwereraninso mlandu wanga ngwolungama.
30
Kodi pali chosalungama palilime panga? Ngati sindizindikira zopanda pake m'kamwa mwanga?
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42