bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 31
Job 31
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 32 →
1
Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?
2
Pakuti gawo la Mulungu lochokera kumwamba, ndi cholowa cha Wamphamvuyonse chochokera m'mwambamo nchiyani?
3
Si ndizo chionongeko cha wosalungama, ndi tsoka la ochita mphulupulu?
4
Nanga sapenya njira zanga, ndi kuwerenga moponda mwanga monse?
5
Ngati ndinayanjana nalo bodza, ndi phazi langa linathamangira chinyengo;
6
andiyese ndi muyeso wolingana, kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.
7
Ngati phazi langa linapatuka m'njira, ndi mtima wanga unatsata maso anga? Ngati chilema chamamatira manja anga?
8
Ndibzale ine nadye wina, ndi zondimerera ine zizulidwe.
9
Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,
10
mkazi wanga aperere wina; wina namuike kumbuyo.
11
Pakuti icho ndi choipitsitsa, ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake.
12
Pakuti ndicho moto wakunyeka mpaka chionongeko, ndi chakuzula zipatso zanga zonse.
13
Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga, potsutsana nane iwo,
14
ndidzatani ponyamuka Mulungu? Ndipo pondizonda Iye ndidzamnyankha chiyani?
15
Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenge iyenso? Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?
16
Ngati ndakaniza aumphawi chifuniro chao, kapena kutopetsa maso a amasiye,
17
kapena kudya nthongo yanga ndekha, osadyako mwana wamasiye;
18
(pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate; ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye chibadwire ine.)
19
Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda chovala, kapena kuti wosowa alibe chofunda;
20
ngati ziuno zake sizinandiyamika, ngati sanafunde ubweya wa nkhosa zanga;
21
ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa, popeza ndinaona thandizo langa kuchipata;
22
libanthuke phewa langa paphalo, ndi dzanja langa liduke pagwangwa.
23
Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa, ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu.
24
Ngati ndayesa golide chiyembekezo changa, ndi kunena ndi golide woyengetsa, ndiwe chikhazikitso changa;
25
ngati ndinakondwera popeza chuma changa nchachikulu, ndi dzanja langa lapeza zochuluka;
26
ngati ndalambira dzuwa lilikuwala, kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;
27
ndi mtima wanga wakopeka m'tseri, ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;
28
ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wake; pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.
29
Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida, kapena kudzitukula pompeza choipa;
30
ndithu sindinalola m'kamwa mwanga muchimwe, kupempha motemberera moyo wake.
31
Ngati amuna a m'hema mwanga sanati, ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?
32
Mlendo sakagona pakhwalala, koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.
33
Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu, ndi kubisa mphulupulu yanga m'chifuwa mwanga;
34
popeza ndinaopa unyinji waukulu, ndi chipepulo cha mafuko chinandiopsetsa; potero ndinakhala chete osatuluka pakhomo panga.
35
Ha! Ndikadakhala naye wina wakundimvera, chizindikiro changa sichi, Wamphamvuyonse andiyankhe; mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wanga!
36
Ndithu ndikadawasenza paphewa panga, ndi kudzimangirira awa ngati korona.
37
Ndikadamfotokozera chiwerengo cha mopondamo mwanga, ndikadamsenderera Iye ngati kalonga.
38
Ngati minda yanga ifuula monditsutsa, ndi nthumbira zake zilira pamodzi;
39
ngati ndadya zipatso zake wopanda ndalama. Kapena kutayitsa eni ake moyo wao;
40
imere minga m'malo mwa tirigu, ndi dawi m'malo mwa barele. Mau a Yobu atha.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42