bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 9
Job 9
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 10 →
1
Pamenepo Yobu anayankha, nati,
2
Zoona, ndidziwa kuti chili chotero. Koma munthu adzakhala wolungama bwanji kwa Mulungu?
3
Akafuna Iye kutsutsana naye, sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa chikwi.
4
Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?
5
Ndiye amene asuntha mapiri, osachidziwa iwo, amene amagubuduza mu mkwiyo wake.
6
Amene agwedeza dziko lapansi lichoke m'malo mwake, ndi mizati yake injenjemere.
7
Amene alamulira dzuwa ndipo silituluka, nakomera nyenyezi chizindikiro chakuzitsekera.
8
Woyala thambo yekha, naponda pa mafunde a panyanja.
9
Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe, ndi Kumpotosimpita.
10
Wochita zazikulu zosasanthulika, ndi zodabwitsa zosawerengeka.
11
Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya; napitirira, koma osamzindikira ine.
12
Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani? Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani?
13
Mulungu sadzabweza mkwiyo wake; athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.
14
Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji, ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye?
15
Ameneyo, chinkana ndikadakhala wolungama, sindikadamyankha; ndikadangompembedza wondiweruza ine.
16
Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.
17
Pakuti andithyola ndi mkuntho, nachulukitsa mabala anga kopanda chifukwa.
18
Sandilola kuti ndipume, koma andidzaza ndi zowawa.
19
Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu? Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani?
20
Chinkana ndikhala wolungama, pakamwa panga padzanditsutsa; chinkana ndikhala wangwiro, padzanditsutsa wamphulupulu.
21
Chinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini, ndipeputsa moyo wanga.
22
Kuli chimodzimodzi monsemo, m'mwemo ndikuti Iye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi.
23
Mkwapulo ukapha modzidzimutsa, adzaseka tsoka la wosachimwa.
24
Dziko lapansi laperekedwa m'dzanja la woipa; aphimba maso a oweruza ake. Ngati sindiye, pali yaninso?
25
Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma; athawa osaona chokoma.
26
Apitirira ngati zombo zaliwiro; ngati mphungu igudukira chakudya chake.
27
Ndikati, Ndidzaiwala chondidandaulitsa, ndidzasintha nkhope yanga yachisoni, ndidzasekerera.
28
Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse, ndidziwa kuti simudzandiyesa wosachimwa.
29
Mlandu udzanditsutsa; potero ndigwire ntchito chabe chifukwa ninji?
30
Ndikasamba madzi a chipale chofewa ndi kuyeretsa manja anga ndi sopo.
31
Mudzandiviikanso muli zoola, ndi zovala zanga zidzanyansidwa nane.
32
Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe. Kuti tikomane mlandu.
33
Palibe wakutiweruza, wakutisanjika ife tonse awiri manja ake.
34
Andichotsere ndodo yake, choopsa chake chisandichititse mantha;
35
kuti ndinene, osamuopa, pakuti sinditero monga umo ndili.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42