bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 36
Job 36
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 37 →
1
Elihu anabwereza, nati,
2
Mundilole pang'ono, ndidzakuuzani, pakuti ndili naonso mau akunenera Mulungu.
3
Ndidzatenga nzeru zanga kutali, ndidzavomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama.
4
Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza, wakudziwitsa mwangwiro ali nanu.
5
Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu, ndipo sapeputsa munthu; mphamvu ya nzeru zake ndi yaikulu.
6
Sasunga woipa akhale ndi moyo, koma awaninkha ozunzika zowayenera iwo.
7
Sawachotsera wolungama maso ake, koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.
8
Ndipo akamangidwa m'nsinga, nakakodwa ndi zingwe za mazunzo,
9
pamenepo awafotokozera ntchito zao, ndi zolakwa zao, kuti anachita modzikuza.
10
Awatseguliranso m'khutu mwao kuti awalangize, nawauza abwerere kuleka mphulupulu.
11
Akamvera ndi kumtumikira, adzatsiriza masiku ao modala, ndi zaka zao mokondwera.
12
Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga, nadzatsirizika osadziwa kanthu.
13
Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo, akawamanga Iye, safuulira.
14
Iwowa akufa akali biriwiri, ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa.
15
Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwake, nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao.
16
Inde akadakukopani muchoke posaukira, mulowe kuchitando kopanda chopsinja; ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.
17
Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa, zolingirirazo ndi chiweruzo zidzakugwiranibe.
18
Pakuti muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo; ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli.
19
Chuma chanu chidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika, kapena mphamvu yanu yonse yolimba?
20
Musakhumbe usiku, umene anthu alikhidwe m'malo mwao.
21
Chenjerani, musalunjike kumphulupulu; pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.
22
Taonani, Mulungu achita mokwezeka mu mphamvu yake, mphunzitsi wakunga Iye ndani?
23
Anamuikira njira yake ndani? Adzati ndani, Mwachita chosalungama?
24
Kumbukirani kuti mukuze ntchito zake zimene anaziimbira anthu.
25
Anthu onse azipenyerera, anthu aziyang'anira kutali.
26
Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
27
Pakuti akweza madontho a mvula, akhetsa mvula ya m'nkhungu yake
28
Imene mitambo itsanulira, nivumbitsira anthu mochuluka.
29
Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo, ndi kugunda kwa msasa wake?
30
Taonani, Iye ayala kuunika kwake pamenepo. Navundikira kunsi kwake kwa nyanja.
31
Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu apatsa chakudya chochuluka.
32
Akutidwa manja ake ndi mphezi, nailamulira igwere pofunapo Iye.
33
Kugunda kwake kulalikira za Iye, zoweta zomwe zilota mtambo woyandikira.
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 37 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42