bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 15
Job 15
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 16 →
1
Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2
Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika, ndi kudzaza mimba yake ndi mphepo ya kum'mawa?
3
Kodi atsutsane ndi mnzake ndi mau akusathandiza? Kapena ndi maneno akusaphindulitsa?
4
Zedi uyesa chabe mantha, nuchepsa chilingiriro pamaso pa Mulungu.
5
Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako, nusankha lilime la ochenjerera.
6
Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai. Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa.
7
Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?
8
Kodi unamva uphungu wachinsinsi wa Mulungu? Ndipo unadzikokera nzeru kodi?
9
Udziwa chiyani, osachidziwa ife? Uzindikira chiyani, chosakhala mwa ife?
10
Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa, akuposa atate wako masiku ao.
11
Masangalatso a Mulungu akuchepera kodi? Kapena uli nacho chinsinsi kodi?
12
Mtima wako usonthokeranji nawe? Maso ako aphethiraphethira chifukwa ninji?
13
Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, ndi kulola mau otere atuluke m'kamwa mwako.
14
Munthu nchiyani kuti akhale woyera, wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?
15
Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake; ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pake.
16
Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi.
17
Ndidzakuonetsa, undimvere; chimene ndinachiona, ndidzakufotokozera;
18
chimene adachinena anzeru, adachilandira kwa makolo ao, osachibisa;
19
ndiwo amene analandira okha dzikoli, wosapita mlendo pakati pao.
20
Munthu woipa adzipweteka masiku ake onse, ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.
21
M'makutu mwake mumveka zoopsetsa; pali mtendere amfikira wakumuononga.
22
Sakhulupirira kuti adzatulukamo mumdima, koma kuti lupanga limlindira.
23
Ayendayenda ndi kufuna chakudya, nati, Chilikuti? Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima.
24
Nsautso ndi chipsinjo zimchititsa mantha, zimlaka ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo.
25
Pakuti amtambasula dzanja lake moyambana ndi Mulungu, napikisana ndi Wamphamvuyonse.
26
Amthamangira Iye mwaliuma, ndi zikopa zake zochindikira.
27
Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake, nachita mafunyenye a mafuta m'zuuno zake;
28
adzakhala m'midzi yopasuka, m'nyumba zosakhalamo munthu, zoti zisandulika muunda.
29
Sadzakhala wolemera, ndi chuma chake sichidzakhalitsa, ndi zipatso zake sizidzachuluka padziko.
30
Sadzachoka mumdima; lawi la moto lidzaumitsa nthambi zake; ndipo adzachoka ndi mpumo wa m'kamwa mwake.
31
Asatame zopanda pake, kudzinyenga nazo; pakuti zopanda pake zidzakhala chombwezera chake.
32
Chidzachitika isanadze nthawi yake; pakuti nthambi yake siidzaphuka.
33
Adzayoyoka zipatso zake zosapsa ngati mpesa, nadzathothoka maluwa ake ngati mtengo wa azitona.
34
Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala chumba, ndi moto udzapsereza mahema a olandira chokometsera mlandu.
35
Aima ndi chovuta, nabala mphulupulu, ndi m'mimba mwao mukonzeratu chinyengo.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42