bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 32
Job 32
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 33 →
1
Pamenepo amuna atatuwa analeka kumyankha Yobu; pakuti anali wolungama pamaso pake pa iye mwini.
2
Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi, wa chibale cha Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.
3
Adapsa mtima pa mabwenzi ake atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa.
4
Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.
5
Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.
6
Ndipo Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi anayankha, nati, Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba; chifukwa chake ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.
7
Ndinati, Amisinkhu anene, ndi a zaka zochuluka alangize nzeru.
8
Koma m'munthu muli mzimu, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.
9
Akulu sindiwo eni nzeru, ndi okalamba sindiwo ozindikira chiweruzo.
10
Chifukwa chake ndinati, Ndimvereni ine, inenso ndidzaonetsa monga umo ndayesera ine.
11
Taonani, ndinalindira mau anu, ndinatcherera khutu zifukwa zanu, pofunafuna inu ponena.
12
Inde ndinasamalira inu; koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu, kapena wakumbwezera mau pakati pa inu.
13
Msamati, Tapeza nzeru ndife, Mulungu akhoza kumkhulula, si munthu ai;
14
popeza sanandiponyere ine mau, sindidzamyankha ndi maneno anu.
15
Asumwa, sayankhanso, Anawathera mau.
16
Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo, popeza akhala duu osayankhanso?
17
Ndidzayankha inenso mau anga, ndidzaonetsa inenso za m'mtima mwanga.
18
Pakuti ndadzazidwa ndi mau, ndi mzimu wa m'kati mwanga undifulumiza.
19
Taonani, m'chifuwa mwanga muli ngati vinyo wosowa popungulira, ngati matumba atsopano akuti aphulike.
20
Ndidzanena kuti chifundo chitsike; ndidzatsegula milomo yanga ndi kuyankha.
21
Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu, kapena kumtchula munthu maina omdyola nao;
22
pakuti sindidziwa kutchula maina osyasyalika; ndikatero Mlengi wanga adzandichotsa msanga.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42