bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 19
Job 19
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 20 →
1
Koma Yobu anayankha, nati,
2
Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti, ndi kundithyolathyola nao mau?
3
Kakhumi aka mwandichititsa manyazi; mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.
4
Ndipo ngati ndalakwa ndithu, kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.
5
Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine, ndi kunditchulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao.
6
Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga, nandizinga ndi ukonde wake.
7
Taonani, ndifuula kuti, Chiwawa! Koma sandimvera; ndikuwa, koma palibe chiweruzo.
8
Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko, naika mdima poyendapo ine.
9
Anandivula ulemerero wanga, nandichotsera korona pamutu panga.
10
Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu; nachizula chiyembekezo changa ngati mtengo.
11
Wandiyatsiranso mkwiyo wake, nandiyesera ngati wina wa adani ake.
12
Ankhondo ake andidzera pamodzi, nandiundira njira yao, nandimangira misasa pozinga hema wanga.
13
Iye anandichotsera abale anga kutali, ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse.
14
Anansi anga andisowa, ndi odziwana nane bwino andiiwala.
15
Iwo a m'nyumba mwanga ndi adzakazi anga andiyesa mlendo; ndine wachilendo pamaso pao.
16
Ndikaitana kapolo wanga, sandibwezera mau, chinkana ndimpembedza pakamwa panga.
17
Mpweya wanga unyansira mkazi wanga, chinkana ndinampembedza ndi kutchula ana a thupi langa.
18
Angakhale ana ang'ono andipeputsa, ndikanyamuka, andinena;
19
mabwenzi anga enieni onse anyansidwa nane; ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga.
20
Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga.
21
Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.
22
Mundilondola bwanji ngati Mulungu, losakukwanirani thupi langa?
23
Ha! Akadalembedwa mau anga! Ha! Akadalembedwa m'buku!
24
Akadawazokota pathanthwe chikhalire, ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu!
25
Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo, nadzauka potsiriza pafumbi.
26
Ndipo khungu langa litaonongeka, pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu,
27
amene ndidzampenya ndekha, ndi maso anga adzamuona, si wina ai. Imso zanga zatha m'kati mwanga.
28
Mukati, Tiyeni timlondole! Popeza chifukwa cha mlandu chapezeka mwa ine;
29
muchite nalo mantha lupanga; pakuti mkwiyo utenga zolakwa za lupanga, kuti mudziwe pali chiweruzo.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42