bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 39
Job 39
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 40 →
1
Kodi udziwa nyengo yakuswana zinkhoma? Kodi wapenyerera pakuswa mbawala?
2
Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira, kapena udziwa nyengo yoti ziswane?
3
Zithuntha, ziswa, zitaya zowawa zao.
4
Ana ao akhala ojincha, akulira kuthengo, achoka osabwerera kwa amao.
5
Ndani walola mbidzi ituluke yaufulu? Anaimasulira mbidzi nsinga zake ndani,
6
imene ndachiyesa chipululu nyumba yake, ndi dziko lakhulo pokhala pake?
7
Aseka phokoso la kumudzi, osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m'goli.
8
Poyenda ponse pamapiri mpa busa pake; ilondola chachiwisi chilichonse.
9
Kodi njati idzavomera kukutumikira, idzakhala ku chodyetseramo chako kodi?
10
Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lake ilime m'mchera? Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa?
11
Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yake njaikulu? Udzaisiyira ntchito yako kodi?
12
Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako, ndi kuzisonkhanitsira kudwale?
13
Phiko la nthiwatiwa likondwera, koma mapiko ndi nthenga zake nzofatsa kodi?
14
Pakuti isiya mazira ake panthaka, nimafunditsa m'fumbi,
15
niiwala kuti phazi lingawaphwanye, kapena chilombo chingawapondereze.
16
Iumira mtima ana ake monga ngati sali ake; idzilemetsa ndi ntchito chabe, popeza ilibe mantha;
17
pakuti Mulungu anaimana nzeru, ndipo sanaigawire luntha.
18
Ikafika nthawi yake, iweramuka, iseka kavalo ndi wa pamsana pake.
19
Wampatsa kavalo mphamvu yake kodi? Wamveka pakhosi pake chenjerere chogwedezeka?
20
Wamlumphitsa kodi ngati dzombe? Ulemerero wa kumina kwake ngwoopsa.
21
Apalasa kuchigwa, nakondwera nayo mphamvu yake; atuluka kukomana nao eni zida.
22
Aseka mantha osaopsedwa, osabwerera kuthawa lupanga.
23
Phodo likuti kochokocho panthiti pake, mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe.
24
Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka, osaimitsika pomveka lipenga.
25
Pomveka lipenga akuti, Hee! Anunkhiza nkhondo ilikudza kutali, kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza.
26
Kodi kabawi auluka mwa nzeru zako, natambasula mapiko ake kunka kumwera?
27
Kodi chiombankhanga chikwera m'mwamba pochilamulira iwe, nichimanga chisanja chake m'mwamba?
28
Kwao nku thanthwe, chigona komweko, pansonga pa thanthwe pokhazikikapo.
29
Pokhala kumeneko chiyang'ana chakudya; maso ake achipenyetsetsa chili kutali.
30
Ana ake akumwa mwazi, ndipo pomwe pali ophedwa, apo pali icho.
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 40 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42