bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 33
Job 33
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 34 →
1
Komatu, Yobu, mumvere maneno anga, mutcherere khutu mau anga.
2
Taonani tsono, ndatsegula pakamwa panga, lilime langa lanena m'kamwa mwanga.
3
Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga, ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.
4
Mzimu wa Mulungu unandilenga, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.
5
Ngati mukhoza, mundiyankhe; mulongosolere mau anu pamaso panga, mukonzeke.
6
Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu; inenso ndinaumbidwa ndi dothi.
7
Taonani, kuopsa kwanga simudzachita nako mantha; ndi ichi ndikusenzetsani sichidzakulemererani.
8
Zedi mwanena m'makutu mwanga, ndinamvanso mau a kunena kwanu, akuti,
9
Ndine woyera ine, wopanda kulakwa, ndine wosapalamula, ndilibe mphulupulu.
10
Taonani, Iye apeza zifukwa zoti anditsutse nazo, andiyesa mdani wake;
11
amanga mapazi anga m'zigologolo, ayang'anira poyenda ine ponse.
12
Taonani, ndidzakuyankhani m'mene muli mosalungama; pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.
13
Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji? Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa.
14
Pakuti Mulungu alankhula kamodzi, kapena kawiri, koma anthu sasamalira.
15
M'kulota, m'masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama,
16
pamenepo atsegula makutu a anthu, nakomera chizindikiro chilangizo chao;
17
kuti achotse munthu ku chimene akadachita, ndi kubisira munthu kudzikuza kwake;
18
kuti amletse angaonongeke, ndi moyo wake ungatayike ndi lupanga.
19
Alangidwanso ndi zowawa pakama pake, ndi kulimbana kowawa kosapuma m'mafupa ake.
20
M'mwemo mtima wake uchita mseru ndi mkate, ndi moyo wake pa chakudya cholongosoka.
21
Mnofu wake udatha, kuti sungapenyeke; ndi mafupa ake akusaoneka atuluka.
22
Inde wasendera kufupi kumanda, ndi moyo wake kwa akuononga.
23
Akakhala kwa iye mthenga, womasulira mau mmodzi mwa chikwi, kuonetsera munthu chomuyenera;
24
pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati, Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo.
25
Mnofu wake udzakhala see, woposa wa mwana; adzabwerera kumasiku a ubwana wake.
26
Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima; m'mwemo aona nkhope yake mokondwera; ndipo ambwezera munthu chilungamo chake.
27
Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindula nako.
28
Koma anandiombola ndingatsikire kumanda, ndi moyo wanga udzaona kuunika.
29
Taona, izi zonse azichita Mulungu kawiri katatu ndi munthu,
30
kumbweza angalowe kumanda, kuti kuunika kwa moyo kumuwalire.
31
Tcherani khutu, Yobu, mundimvere ine; mukhale chete, ndipo ndidzanena ine.
32
Ngati muli nao mau mundiyankhe. Nenani, pakuti ndifuna kukulungamitsani.
33
Ngati mulibe mau, tamverani ine; mukhale chete, ndipo ndidzakuphunzitsani nzeru.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42