bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 30
Job 30
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 31 →
1
Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka, iwo amene atate ao ndikadawapeputsa, osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga.
2
Mphamvunso ya m'manja mwao ndikadapindulanji nayo? Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha,
3
atsala mafupa okhaokha ndi kusowa ndi njala; akungudza nthaka youma kuli mdima wa m'chipululu chopasuka.
4
Atchera therere lokolera kuzitsamba, ndi chakudya chao ndicho mizu ya dinde.
5
Anawapirikitsa pakati pa anthu, awafuulira ngati kutsata mbala.
6
Azikhala m'zigwa za chizirezire, m'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga.
7
Pakati pa zitsamba alira ngati bulu, pansi pa khwisa asonkhana pamodzi.
8
Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina; anawaingitsa kuwachotsa m'dziko.
9
Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo, nandiyesa nthanthi.
10
Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine, saleka kuthira malovu pankhope panga.
11
Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza; anataya chomangira m'kamwa mwao pamaso panga.
12
Kudzanja langa lamanja anauka oluluka, akankha mapazi anga, andiundira njira zao zakundiononga.
13
Aipsa njira yanga, athandizana ndi tsoka langa; ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi.
14
Akudza ngati opitira pogamuka linga papakulu, pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine.
15
Anditembenuzira zondiopsa, auluza ulemu wanga ngati mphepo; ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo.
16
Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m'kati mwanga; masiku akuzunza andigwira.
17
Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine, ndi zowawa zondikungudza sizipuma.
18
Mwa mphamvu yaikulu ya nthenda yanga chovala changa chinasandulika, chindithina ngati pakhosi pa malaya anga.
19
Iye anandiponya m'matope, ndipo ndafanana ndi fumbi ndi phulusa.
20
Ndifuula kwa Inu, koma simundiyankha; ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera.
21
Mwasandulika kundichitira nkharwe; ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza.
22
Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo; ndipo mundisungunula mumkuntho.
23
Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa, ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse.
24
Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lake kodi? Akati aonongeke, safuulako kodi?
25
Kodi sindinamlirira misozi wakulawa zowawa? Kodi moyo wanga sunachitira chisoni osowa?
26
Muja ndinayembekeza chokoma chinadza choipa, ndipo polindira kuunika unadza mdima.
27
M'kati mwanga mupweteka mosapuma, masiku a mazunzo andidzera.
28
Ndiyenda ndili wothimbirira osati ndi dzuwa ai; ndinyamuka mumsonkhano ndi kufuula.
29
Ndili mbale wao wa ankhandwe, ndi mnansi wao wa nthiwatiwa.
30
Khungu langa lada, nilindifundukira; ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.
31
Chifukwa chake zeze wanga wasandulika wa maliro, ndi chitoliro changa cha mau a olira misozi.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42