bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 29
Job 29
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 30 →
1
Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati,
2
Ha! Ndikadakhala monga m'miyezi yapitayi, monga m'masiku akundisunga Mulungu;
3
muja nyali yake inawala pamutu panga, ndipo ndi kuunika kwake ndinayenda mumdima;
4
monga umo ndinakhala m'masiku anga olimba, muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga.
5
Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi, ndi ana anga anandizinga;
6
muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka, ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta a azitona!
7
Muja ndinatuluka kunka kuchipata kumudzi, muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,
8
anyamata anandiona nabisala, okalamba anandinyamukira, nakhala chilili.
9
Akalonga anadziletsa kulankhula, ndi kugwira pakamwa pao;
10
mau a omveka anali zii, ndi lilime lao linamamatira kumalakalaka ao.
11
Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa; ndipo pondiona diso, linandichitira umboni.
12
Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakufuula; mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi.
13
Dalitso la iye akati atayike linandidzera, ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera.
14
Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine; chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.
15
Ndinali maso a akhungu, ndi mapazi a otsimphina.
16
Ndinali atate wa waumphawi; ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwa ndinafunsitsa.
17
Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama, ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake.
18
Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'chisa changa; ndipo ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.
19
Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi; ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.
20
Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine, ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m'dzanja mwanga.
21
Anthu anandimvera, nalindira, nakhala chete, kuti ndiwapangire.
22
Nditanena mau anga sanalankhulenso, ndi kunena kwanga kunawakhera.
23
Anandilindira ngati kulindira mvula, nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika.
24
Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima; ndipo sanagwetse kusangalala kwa nkhope yanga.
25
Ndinawasankhira njira yao ndi kukhala mkulu wao. Ndinakhala ngati mfumu mwa ankhondo ake, ngati wotonthoza ofedwa.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42