bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 38
Job 38
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 39 →
1
Pamenepo Yehova anayankha Yobu m'kamvulumvulu, nati,
2
Ndani uyu adetsa uphungu, ndi mau opanda nzeru?
3
Udzimangire m'chuuno tsono ngati mwamuna; ndikufunsa, undidziwitse.
4
Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.
5
Analemba malire ake ndani, popeza udziwa? Anayesapo chingwe chake ndani?
6
Maziko ake anakumbidwa pa chiyani? Kapena anaika ndani mwala wake wa pangodya,
7
muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?
8
Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko, muja idakamula ngati kutuluka m'mimba,
9
muja ndinayesa mtambo chovala chake, ndi mdima wa bii nsalu yake yokulunga,
10
ndi kuilembera malire anga, ndi kuika mipikizo ndi zitseko,
11
ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo; apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?
12
Kodi walamulira m'mawa chiyambire masiku ako, ndi kudziwitsa mbandakucha malo ake;
13
kuti agwire malekezero a dziko lapansi, nakutumule oipa achokeko?
14
Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa chosindikiza, ndi zonse zibuka ngati chovala;
15
ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone, ndi dzanja losamulidwa lithyoledwa.
16
Kodi unalowa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama penipeni?
17
Kodi zipata za imfa zinavumbulukira iwe? Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?
18
Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi? Fotokozera, ngati uchidziwa chonse.
19
Ili kuti njira yomukira pokhala kuunika? Ndi mdima, pokhala pake pali kuti,
20
kuti upite nao kumalire ake, kuti uzindikire miseu ya kunyumba yake?
21
Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo, ndi masiku ako achuluka kuwerenga kwao.
22
Kodi unalowa m'zosungiramo chipale chofewa? Kapena unapenya zosungiramo matalala,
23
amene ndiwasungira tsiku la nsautso, tsiku lakulimbana nkhondo?
24
Njira ili kuti yomukira pogawikana kuunika, kapena pomwazikira mphepo ya kum'mawa pa dziko lapansi?
25
Ndani anachikumbira mchera chimvula, kapena njira ya bingu la mphezi,
26
kuvumbitsa mvula pa dziko lopanda anthu, kuchipululu kosakhala munthu,
27
kukhutitsa thengo la kunkhwangwala, ndi kuphukitsa msipu?
28
Kodi mvula ili naye atate? Kapena wabala ndani madontho a mame?
29
Chipale chinatuluka m'mimba ya yani? Ndi chisanu chochokera m'mwamba anachibala ndani?
30
Madzi aundana ngati mwala, ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi.
31
Kodi ungamange gulu la Nsangwe? Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana?
32
Ungatulutse kodi nyenyezi m'nyengo zao monga mwa malongosoledwe ao? Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ake?
33
Kodi udziwa malemba a kuthambo? Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao pa dziko lapansi?
34
Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo, kuti madzi ochuluka akukute?
35
Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke, ndi kunena nawe, Tili pano?
36
Ndani analonga nzeru m'mitambomo? Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha?
37
Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru, ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani,
38
pokandika fumbi, ndi kuundana zibuma pamodzi?
39
Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama? Ndi kukwaniritsa chakudya cha misona,
40
pamene ibwatama m'ngaka mwao, nikhala mobisala kulaliramo?
41
Amkonzeratu khungubwi chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya?
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 39 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42