bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 28
Job 28
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 29 →
1
Koma kuli mtapo wa siliva, ndi malo a golide amene amuyenga.
2
Chitsulo achitenga m'nthaka, ndi mkuwa ausungunula kumwala.
3
Munthu athawitsa mdima, nafunafuna mpaka malekezero onse, miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.
4
Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu; aiwalika ndi phazi lopitapo; apachikika kutali ndi anthu, nalendewalendewa.
5
Kunena za nthaka, kuchokera momwemo mumatuluka chakudya, ndi m'munsi mwake musandulizika ngati ndi moto.
6
Miyala yake ndiyo malo a safiro, ndipo ili nalo fumbi lagolide.
7
Njira imeneyi palibe chiombankhanga chiidziwa; lingakhale diso la kabawi losapenyapo.
8
Nyama zodzikuza sizinapondapo, ngakhale mkango waukali sunapitapo.
9
Munthu atambasulira dzanja lake kumwala; agubuduza mapiri kuyambira kumizu.
10
Asema njira pakati pa matanthwe, ndi diso lake liona chilichonse cha mtengo wake.
11
Atseka mitsinje ingadonthe; natulutsira poyera chobisikachi.
12
Koma nzeru, idzapezeka kuti? Ndi luntha, malo ake ali kuti?
13
Munthu sadziwa mtengo wake; ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.
14
Pozama pakuti, Mwa ine mulibe; ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.
15
Silipezeka ndi golide, sayesapo siliva mtengo wake.
16
Sailinganiza ndi golide wa Ofiri, ndi sohamu wa mtengo wake wapatali kapena safiro.
17
Golide ndi krustalo sizilingana nayo; ndi kusinthana kwake, siisinthanika ndi zisambiro za golide woyengetsa.
18
Korali kapena ngale sizikumbukikapo. Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira.
19
Topazi wa Kusi sufanana nayo, sailinganiza ndi golide wolongosoka.
20
Koma nzeru ifuma kuti? Ndi luntha, pokhala pake pali kuti?
21
Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse, pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga.
22
Chionongeko ndi Imfa zikuti, Tamva mbiri yake m'makutu mwathu.
23
Mulungu ndiye azindikira njira yake, ndiye adziwa pokhala pake.
24
Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi, naona pansi pa thambo ponse;
25
pamene anaikira mphepo muyeso wake, nayesera madzi miyeso;
26
pakuchitira mvula lamulo, ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;
27
pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera; anaikonza, naisanthula.
28
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42