bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 5
Job 5
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 6 →
1
Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi? Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo?
2
Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.
3
Ndinapenya wopusa woyala mizu; koma pomwepo ndinatemberera pokhala pake.
4
Ana ake akhala otekeseka, napsinjika kuchipata, wopanda wina wakuwapulumutsa.
5
Zokolola zao anjala azidya, azitenga ngakhale kuminga, ndi aludzu ameza chuma chao.
6
Pakuti nsautso sutuluka m'fumbi, ndi mavuto saphuka m'nthaka.
7
Koma munthu abadwira mavuto, monga mbaliwali zikwera ziuluzika.
8
Koma ine ndikadafuna Mulungu, ndikadaikira mlandu wanga Mulungu;
9
amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.
10
Amene avumbitsa mvula panthaka, natumiza madzi paminda;
11
kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka, kuti iwo a maliro akwezedwe kosatekeseka.
12
Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera, kuti manja ao sakhoza kuchita chopangana chao.
13
Akola eni nzeru m'kuchenjera kwao, ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pachabe.
14
Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa, nayambasa dzuwa lili pakati pamtu monga usiku.
15
Apulumutsa aumphawi kulupanga la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu.
16
Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo, ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.
17
Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula; chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse.
18
Pakuti apweteka, namanganso mabala; alasa, ndi manja ake omwe apoletsa.
19
Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.
20
Adzakuombola kuimfa m'njala, ndi kumphamvu ya lupanga m'nkhondo.
21
Udzabisikira mkwapulo wa lilime, sudzachiopanso chikadza chipasuko.
22
Chipasuko ndi njala udzaziseka; ngakhale zilombo za padziko osaziopa.
23
Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala ya kuthengo; ndi nyama za kuthengo zidzakhala nawe mumtendere.
24
Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere; nudzazonda za m'banja mwako osasowapo kanthu.
25
Udzapezanso kuti mbeu zako zidzachuluka, ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.
26
Udzafika kumanda utakalamba, monga abwera nao mtolo wa tirigu m'nyengo yake.
27
Taona, ichi tachifunafuna, chili chotero; uchimvere, nuchidziwire wekha.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42