bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 12
Job 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 13 →
1
Pamenepo Yobu anayankha, nati,
2
Zoonadi inu ndinu anthu, ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.
3
Koma inenso ndili nayo nzeru monga inu. Sindingakuchepereni; ndani sadziwa zonga izi?
4
Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa.
5
Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwake, limlindira woterereka mapazi ake.
6
Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao.
7
Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza, ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza.
8
Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza; ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera.
9
Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse; kuti dzanja la Yehova lichita ichi?
10
M'dzanja mwake muli mpweya wa zamoyo zonse, ndi mzimu wa munthu aliyense.
11
M'khutumu simuyesa mau, monga m'kamwa mulawa chakudya chake?
12
Kwa okalamba kuli nzeru, ndi kwa a masiku ochuluka luntha.
13
Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi luntha ali nazo.
14
Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso; amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira.
15
Taona atsekera madzi, naphwa; awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.
16
Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru. Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ake.
17
Apita nao maphungu atawafunkhira, napulukiritsa oweruza milandu.
18
Amasula chomangira cha mafumu, nawamangira nsinga m'chuuno mwao.
19
Apita nao, ansembe atawafunkhira, nagubuduza amphamvu.
20
Amchotsera wokhulupirika kunena kwake. Nalanda luntha la akulu.
21
Atsanulira mnyozo pa akalonga, nawansezera olimba lamba lao.
22
Avumbulutsa zozama mumdima, natulutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;
23
achulukitsa amitundu, nawaononganso; abalalikitsa amitundu, nawabwezanso.
24
Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao, nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira.
25
Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika, ndipo awayendetsa dzandidzandi.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42