bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Job 20
Job 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 21 →
1
Pamenepo anayankha Zofari Mnaama, nati,
2
M'mwemo zolingirira zanga zindiyankha, chifukwa chake ndifulumidwa m'kati mwanga.
3
Ndamva kudzudzula kwakundichititsa manyazi, ndi mzimu wa nzeru yanga undiyankha.
4
Kodi suchidziwa ichi chiyambire kale lomwe, nuyambira anaika munthu pa dziko lapansi,
5
kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?
6
Chinkana ukulu wake ukwera kunka kuthambo, nugunda pamitambo mutu wake;
7
koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zake; iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?
8
Adzauluka ngati loto, osapezekanso; nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku.
9
Diso lidamuonalo silidzamuonanso; ndi malo ake sadzampenyanso.
10
Ana ake adzapempha aumphawi awakomere mtima; ndi manja ake adzabweza chuma chake.
11
Mafupa ake adzala nao unyamata wake, koma udzagona naye pansi m'fumbi.
12
Chinkana choipa chizuna m'kamwa mwake, chinkana achibisa pansi pa lilime lake;
13
chinkana achisunga, osachileka, nachikhalitsa m'kamwa mwake;
14
koma chakudya chake chidzasandulika m'matumbo mwake, chidzakhala ndulu ya mphiri m'kati mwake.
15
Anachimeza chuma koma adzachisanzanso; Mulungu adzachitulutsa m'mimba mwake.
16
Adzayamwa ndulu ya mphiri; pakamwa pa njoka padzamupha.
17
Sadzapenyerera timitsinje, toyenda nao uchi ndi mafuta.
18
Chimene adagwiriracho ntchito, adzachibweza, osachimeza; sadzakondwera monga mwa zolemera zake adaziona.
19
Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi; analanda nyumba mwachiwawa, imene sanaimange.
20
Popeza sanadziwe kupumula m'kati mwake, sadzalanditsa kanthu ka zofunika zake.
21
Sikunatsalira kanthu kosadya iye, chifukwa chake zokoma zake sizidzakhalitsa.
22
Pomkwanira kudzala kwake adzakhala m'kusauka; dzanja la yense wovutika lidzamgwera.
23
Poti adzaze mimba yake, Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali, nadzamvumbitsira uwu pakudya iye.
24
Adzathawa chida chachitsulo, ndi muvi wa uta wamkuwa udzampyoza.
25
Auzula, nutuluka m'thupi mwake; inde nsonga yonyezimira ituluka m'ndulu mwake; zamgwera zoopsa.
26
Zamdima zonse zimsungikira zikhale chuma chake, moto wosaukoleza munthu udzampsereza; udzatha wotsalira m'hema mwake.
27
M'mwamba mudzavumbulutsa mphulupulu yake, ndi dziko lapansi lidzamuukira.
28
Phindu la m'nyumba mwake lidzachoka, akatundu ake adzamthawa tsiku la mkwiyo wake.
29
Ili ndi gawo la munthu woipa, lochokera kwa Mulungu, ndi cholowa amuikiratu Mulungu.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42