bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 1
Job 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 2 →
1
Kudaali munthu wina, dzina lake Yobe, amene ankakhala m'dziko la Uzi. Munthu ameneyo anali wosalakwa ndiponso wolungama. Ankaopa Mulungu namapewa zoipa.
2
Anali ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri, ndi ana aakazi atatu.
3
Anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ng'ombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500. Anali ndi antchito ambiri, choncho anali munthu wotchuka koposa anthu onse a m'maiko akuvuma.
4
Ana ake aamuna ankachita phwando mosinthana, tsiku lina kwa wina, tsiku lina kwa wina. Ndipo ankaitana alongo ao atatu aja ku maphwando aowo.
5
Tsono masiku a phwandowo akatha, Yobe ankadzuka m'mamaŵa napereka nsembe, kuperekera mwana aliyense, kuti anawo ayeretsedwe potsata malamulo a chipembedzo. Yobeyo ankati, “Mwina mwake, wina mwa ana angaŵa adachimwa, adatukwana Mulungu mumtima mwake.” Umu ndimo m'mene ankachitira Yobe nthaŵi zonse.
6
Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi.
7
Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.”
8
Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wazindikirapo mtumiki wanga Yobe, kuti safanafana ndi wina aliyense pa dziko lapansi? Iye uja ndi munthu wosalakwa ndi wolungama. Amandimvera Ine Mulungu, ndipo amapewa zoipa.”
9
Satana adafunsa Chauta kuti, “Kani mwayesa Yobe uja amangokumverani pachabe?
10
Suja Inu mwakhala mukumteteza ponseponse iye uja, pamodzi ndi banja lake ndi zinthu zake zonse zimene ali nazo. Mudamdalitsanso pa ntchito zimene amachita, ndipo chuma chake nchochuluka kwambiri m'dzikomo.
11
Koma tsopano tangoyesani kumchotsera zonse zimene ali nazo, muwona, adzakutukwanirani pamaso.”
12
Chauta adauza Satana kuti, “Chabwino, zonse zimene Yobe ali nazo ndaziika m'manja mwako. Koma iye yekhayo usamkhudze.” Pamenepo Satanayo adachoka, kumsiya Chauta.
13
Tsiku lina ana aamuna ndi ana aakazi a Yobe ankachita phwando m'nyumba mwa mkulu wao.
14
Ndiye kudafika wamthenga kwa Yobe kudzamuuza kuti, “Ng'ombe zinalikulima, ndipo abulu analikudya pafupi pomwepo.
15
Mwadzidzidzi nkubwera Aseba kudzatithira nkhondo nalanda ng'ombezo ndi abulu omwe. Ndipo apha antchito onse, koma ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”
16
Iyeyo akulankhulabe, padafikanso wina, nati, “Kunagwa mphezi ndipo yapsereza nkhosa zonse pamodzi ndi abusa omwe, onse psiti. Ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”
17
Ameneyu asanatsirize kulankhula, padafikanso wina, nati, “Kunafika magulu atatu a Akaldeya kudzatithira nkhondo. Atilanda ngamira zonse, ndipo apha antchito onse. Ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.”
18
Iyeyo mau akali m'kamwa, padafikanso wina, nati, “Ana anu onse anali pa phwando m'nyumba ya mkulu wao.
19
Mwadzidzidzi chayamba chimphepo champhamvu chochokera ku chipululu, nkudzaomba nyumbayo mbali zonse. Motero yagwa ndi kuŵapsinja anawo. Onse aphedwa, ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.”
20
Yobe atamva zimenezo, adadzambatuka, nkung'amba zovala zake. Adameta tsitsi, ndipo adadzigwetsa pansi napembedza Mulungu.
21
Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”
22
Ngakhale zidaayenda motero, Yobe sadachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.”
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42