bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 12
Job 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 13 →
1
Yobe adayankha kuti,
2
“Inunso ndinu anthu, ndipo mukafa, nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi.
3
Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu nomwe. Inu simundipambana, ai. Aliyense amadziŵa zonse mwanenazi.
4
Ine ndine chinthu choseketsa kwa abwenzi anga. Ine amene ndinkapemphera kwa Mulungu, Iye nkundiyankha, ine munthu wolungama ndi wopanda mlandu, tsopano ndine chinthu chochiseka.
5
Munthu amene ali pabwino amanyoza mnzake amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.
6
Achifwamba ndiwo amakhala pa mtendere, amene amaputa Mulungu ndiwo amakhala pabwino. Anthuwo amadalira nyonga zao ngati ndiye Mulungu wao.
7
“Koma ufunse kwa nyama zakuthengo, zidzakuphunzitsa. Ufunse mbalame zamumlengalenga, zidzakuuza.
8
Upemphe nzeru kwa zolengedwa za dziko lapansi, zidzakuphunzitsa, ngakhale nsomba zam'nyanja zidzakufotokozera.
9
Kodi mwa zonsezo nchiti chimene sichidziŵa kuti zonsezi adachita ndi Chauta?
10
M'manja mwake ndimo muli zamoyo zonse, mulinso moyo wa anthu a mitundu yonse.
11
Kodi suja khutu ndiye limamva mau, monga m'mene lilime ndiye limalaŵa chakudya?
12
Inde anthu okalamba ali ndi nzeru, anthu amvulazakale ndi omvetsa zinthu.
13
“Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana. Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse.
14
Akapasula, palibe woti nkumanganso. Akatsekera munthu m'ndende, palibe woti nkumtsekulira.
15
Akamanga mvula, dziko limauma, Akaimasula, madzi amasefukira pa dziko lonse.
16
Iye ali ndi mphamvu, ndiponso ali ndi nzeru zonse. Anthu opusitsidwa, ndiponso opusitsa anzao, onsewo ali mu ulamuliro wake.
17
Iye amalanda aphungu nzeru zao, ndipo amapusitsa aweruzi.
18
Amamasula am'ndende a mafumu, ndipo amaŵamanga mafumuwo.
19
Amasokeza ansembe ataŵalanda nzeru zao, ndipo amatsitsa atsogoleri amphamvu.
20
Amakhalitsa chete aphungu okhulupirika, ndipo akuluakulu amaŵalanda luntha.
21
Amanyoza anthu otchuka, ndipo anthu anyonga amaŵatha mphamvu.
22
Amavundukula zamumdima, ndipo mdimawo amausandutsa kuŵala.
23
Amakuza mitundu ina ya anthu, koma inanso amaiwononga. Amachulukitsa mafuko, nkuŵamwazanso.
24
Amasandutsa atsogoleri kuti akhale zitsiru, ndi kumaŵayendetsa m'thengo mopanda njira.
25
Iwowo amanka nafufuza njira mumdima mopanda kuŵala, nkumayenda ali dzandidzandi ngati oledzera.”
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42