bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 33
Job 33
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 34 →
1
“Koma tsopano inu aYobe, mverani mau anga, mutchere khutu ku zonse zimene ndinene.
2
Tsopano ndiyamba kulankhula, ndikuuzani za mumtima mwanga.
3
Mau anga akusonyeza kulungama kwa mtima wanga, zimene ndimazidziŵa ndimalankhula moona.
4
Mzimu wa Mulungu udandiwumba. Mpweya wa Mphambe udandipatsa moyo.
5
Mundiyankhe ngati mungathe. Mulankhule mau anu tsatanetsatane pamaso panga, konzekani tsono.
6
Kunena zoona, ine ndine mnzanu pamaso pa Mulungu, poti inenso adandiwumba ndi dothi.
7
Musachite mantha ndi kuwopsedwa nane, chifukwa sindikupanikizani koopsa ai.
8
“Zoonadi, ndamva zimene mwalankhula, mau anu ndaŵatsata bwino.
9
Inu mukuti, ‘Ndine woyera mtima, ndilibe cholakwa. Ndine wolungama, ndilibe tchimo.
10
Mulungu wandipeza zifukwa zoti anditsutse nazo, Iye akundiyesa mdani wake.
11
Akumanga mapazi anga m'zigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’
12
“Inu aYobe simukukhoza pa zimenezi, popeza kuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.
13
Chifukwa chiyani mukulimbana ndi Mulungu nkumanena kuti, ‘Pa mau angaŵa sadzayankhapo ndi amodzi omwe?’
14
Pajatu Mulungu amalankhula mwa njira zosiyanasiyana, koma anthu sazindikira zimenezo.
15
M'maloto, m'masomphenya usiku, pamene anthu ali m'tulo tofa nato, pamene akungosinza chabe pa bedi,
16
pamenepo amaŵatsekula makutu anthuwo, naŵaopsa ndi machenjezo.
17
Mulungu amachita izi kuti amletse munthu zoipa zimene amachita, amafuna kuthetseratu kunyada kwake.
18
Amalanditsa munthu ku manda, amapulumutsa moyo wake kuti ungaonongeke ndi lupanga.
19
“Mwina Mulungu amalanganso munthu ndi matenda kuti akonzeke, nthaŵiyo thupi lake lonse limangophwanya.
20
Choncho moyo wake umanyansidwa ndi chakudya chomwe, sangadye ngakhale zakudya zabwino.
21
Thupi lake limaonda, osatha kulithira m'maso, ndipo mafupa ake amene kale sankaoneka, amaonekera poyera.
22
Munthuyo akutsikira ku manda, ali pafupi kupita ku malo a anthu akufa.
23
Koma pataoneka mngelo, ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri otere, wodzamkumbutsa zimene zili zoyenera,
24
ngati mngeloyo amkomera mtima, nati, ‘Mpulumutseni kuti asapite ku manda, dipo lake nali,’
25
pamenepo thupi lake lisanduke lasee ngati lapaubwana, ndipo iye abwerere ku masiku a unyamata wake,
26
Tsono munthu amapemphera kwa Mulungu, Iyeyo nkumulandira. Amabwera pamaso pa Mulungu mokondwa, ndipo Mulungu amamchitira zolungama.
27
Apo adzavomera pamaso pa anthu kuti, ‘Ndidachimwa, sindidachite zolungama. Koma Mulungu sadandilange koyenerana ndi kuchimwa kwanga.
28
Iye adandipulumutsa kuti ndisapite ku manda, ndidzaonanso kuŵala kwa dzuŵa!’
29
“Zoonadi, Mulungu amachita zonsezi kaŵirikaŵiri ndi anthu.
30
Amapulumutsa moyo wa munthu ku malo a imfa, kuti athe kuwonanso kuŵala kwa moyo.
31
“Inu aYobe, mutchere khutu, mundimvere ine. Mukhale chete, kuti ine ndilankhule.
32
Ngati muli ndi mau, mundiyankhe. Mulankhule, chifukwa ndifuna kuti mupezeke wolungama.
33
Ngati si choncho, mumvere ine, khalani chete, ndipo ine ndikuphunzitsani nzeru.” Mulungu ndiyedi wolungama.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42