bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 11
Job 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 12 →
1
Tsono Zofari wa ku Naama adayankha kuti,
2
“Kodi mau ambirimbiriŵa nkukhala osaŵayankha? Kodi kulongolola nkumulungamitsa munthu?
3
Iwe Yobe, kodi anthu nkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku? Kodi ukamanyodola, sadzakhalapo wina aliyense wokudzudzula?
4
Iwe umati mau akowo ndi oona, ukuti ndiwe wangwiro pamaso pa Mulungu.
5
Koma ha, achikhala Mulungu adaalankhula, achikhala adaakudzudzula,
6
achikhala adaakuululira zinsinsi za nzeru! Paja Iye uja nzeru zake ndi zozama zedi. Udziŵe tsono kuti Mulungu akukulanga pang'ono, mosalingana nkuchuluka kwa zolakwa zako.
7
“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungathe kudziŵa kukula kwa nzeru za Mphambe?
8
Malire a nzeru zake ali kutali kuposa mlengalenga. Nanga iwe ungachitepo chiyani? Malire a nzeru zake ndi ozama kupitirira dziko la anthu akufa. Nanga iwe ungathe kudziŵapo chiyani?
9
Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana kutalika kwa dziko lapansi, ndi kupingasa kwa nyanja zamchere.
10
Mulungu akabwera nakutsekera m'ndende, ndipo akakutulutsira ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?
11
Mulungu amazindikira anthu abodza. Pamene pali zolakwa, Iye uja nkupanda kudziŵa?
12
Paja amati, Chitsiru nchitsiru ndithu, ndipo nyama ndi nyama ndithu.
13
“Iwe Yobe, mumtima mwako ukhale wolungama, upemphe chifundo kwa Mulungu.
14
Ngati mumtima mwako muli cholakwa, uchichotse, choipa chilichonse chisakhale m'moyo mwako.
15
Ukatero, ndiye kuti manyazi ako onse adzatha, sudzazyolikanso pamaso pa anthu. Mtima wako udzakhazikika, ndipo sudzaopa kalikonse.
16
Zoŵaŵa zakozi udzaziiŵala, zidzakhala ngati madzi amene apita kale.
17
Pamenepo moyo wako udzaŵala kupambana dzuŵa. Usiku udzakhala ngati usana kwa iwe.
18
Udzalimba mtima poti chikhulupiriro chilipo. Mulungu adzakutchinjiriza, ndipo udzapumula mwamtendere.
19
Nthaŵi yogona palibe amene adzakuwopse. Ambiri adzakupempha kuti uŵachitire zabwino.
20
Anthu oipa nawonso adzafunafuna thandizo, koma sadzaona njira yopulumukira, chiyembekezo chao ndi imfa basi.” Yobe
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42