bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 40
Job 40
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 41 →
1
Tsono Chauta adafunsa Yobe kuti,
2
“Kodi munthu wamakaniwe ufuna kukangana ndi Mphambe? Chabwino, iwe amene unatsutsana ndi Mulungu uyankhe zimenezo.”
3
Apo Yobe adayankha Chauta kuti,
4
“Ine sindili kanthu konse! Kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Palibe, koma kungogwira pakamwa.
5
Ndidalankhula kamodzi, sindiyankhanso. Ndidalankhula kaŵiri, sindiwonjezanso kanthu kena.” Mau a Chauta.
6
Tsono Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti,
7
“Tsopano vala dzilimbe ngati mphongo. Ndikufunsa mafunso, iweyo undiyankhe.
8
Kodi ungandiyese ine wolakwa? Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?
9
Kodi uli ndi mphamvu monga Ine Mulungu? Kodi mau ako angagunde monga m'mene amagundira mau anga?
10
“Ngati zili choncho udzipatse ufumu ndiponso ulemu. Uvale ulemerero wachifumu.
11
Tsanyula mkwiyo wako wosefukira, uyang'ane aliyense wodzikuza, ndipo umchepetse.
12
Uyang'ane aliyense wodzikweza, ndipo umtsitse. Oipa onse uŵaponderezere pamalo pomwe aliripo.
13
Onsewo uŵafwirise pamodzi m'chifwilimbwiti. Uŵakulunge kumaso m'dziko la anthu akufa.
14
Ukatero, nanenso ndidzakuvomereza, kuti mphamvu zako zakupambanitsadi.
15
“Taganiza za mvuu, Ine ndidaipanga monga momwe ndidapangira iwe. Imadya udzu ngati ng'ombe.
16
Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga zedi.
17
Imaimiritsa mchira wake kuti tototo, ngati mtengo wa mkungudza. Mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.
18
Mafupa ake ndi olimba ngati misiwe yamkuŵa, nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.
19
“Mvuu ndiyo yaikulu mwa zolengedwa za Ine Mulungu. Ine amene ndidailenga ndidaipatsa maso ake oopsa aja.
20
Imapeza chakudya kumtunda kumene nyama zonse zakuthengo zimaseŵera.
21
Imagona patsinde pa zitsamba za mipeta, imabisalika m'bango ndiponso pa thaŵale.
22
Zitsamba za mipeta ndizo zimaipatsa mthunzi. Misondodzi yamumtsinje imaiphimba.
23
Madzi amumtsinje akamakokoma, iyo sichita mantha. Ngakhale madzi a mu Yordani aiyese m'khosi, sitekeseka nazo.
24
Kodi nanga alipo wina amene angathe kukola mvuu ndi mbedza kapena kuikola mu msampha?
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 41 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42