bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 10
Job 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 11 →
1
“Ndithudi, ndatopa nawo moyo wanga, choncho ndidzalankhula zodandaula zanga momasuka. Ndidzaulula zoŵaŵa zonse zamumtima.
2
Ndidzauza Mulungu kuti, Inu Mulungu, musandiweruze kuti ndine wolakwa. Koma mundidziŵitse chifukwa chimene mukukanganirana nane.
3
Kodi inu zikukukomerani kuti mundizunze ndi kundinyoza ine, ntchito ya manja anune, chonsecho mukukondera upo wa anthu oipa?
4
Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga m'mene amaziwonera munthu?
5
Kodi masiku anu ndi aafupi monga m'mene aliri masiku a munthu? Kodi zaka zanu zili ngati zaka za munthu?
6
Chifukwa chiyani tsono mukufufuza zolakwa zanga? Chifukwa chiyani mukufuna kundipeza mlandu?
7
Koma chonsecho mukudziŵa bwino lomwe kuti ine ndine wosalakwa, kuti palibe ndi mmodzi yemwe amene angandipulumutse m'manja mwanu.
8
“Mudandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Koma tsopano mukufuna kundiwononga ndi manja anu omwewo.
9
Musaiŵale kuti paja mudandipanga ndi dothi. Kodi mukufuna kundibwezeranso kufumbi komweko?
10
Suja mudapatsa bambo wanga mphamvu zoti andibale, suja mudandikuza bwino m'mimba mwa mai wanga?
11
Mudandikuta ndi khungu ndi mnofu, mudalumikiza mafupa anga ndi mitsempha.
12
Mudandipatsa moyo mwa chikondi chanu chosasinthika, mudandisamala bwino kuti moyo wanga ulimbike.
13
Nthaŵi yonseyo munkabisa zolinga zanu. Koma tsopano ndikuŵadziŵa maganizo anu.
14
Munkapenyetsetsa kuti muwone ngati nditi ndichimwe. Munali wosafuna kukhululukira tchimo langa lililonse.
15
Mukandipeza wolakwa, tsoka langa! Ngakhale mundipeze wosalakwa, ndigwetsabe nkhope, pakuti ndagwidwa ndi manyazi, poona mavuto angaŵa.
16
Ndikadzilimbitsa mtima, mumakhala ngati mkango wondisaka, mumafuna kundiwopsa ndi mphamvu zanu.
17
Mumandiikiranso mboni zondineneza, mkwiyo wanu umanka nukulirakulira. Magulu anu olimbana nane akunka nachulukirachulukira.
18
“Inu Mulungu, chifukwa chiyani mudandibadwitsa ineyo? Achikhala ndidaangofa, wina aliyense asanandiwone.
19
Achikhala ndidaachita ngati mtayo basi, akadanditenga pobadwapo nkupita nane ku manda.
20
Kodi masiku a moyo wanga si oŵerengeka chabe? Ingondilekani kuti ndipumuleko pang'ono,
21
ndisanapite kumene sindidzabwerako, dziko la imfa, kumene kuli mdima wandiweyani,
22
ku dziko lamdimatu ndi lachisokonezo, kumene ngakhale kuŵala kudasanduka mdima.” Zofari
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42