bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 34
Job 34
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 35 →
1
Elihu popitiriza kulankhula adati,
2
“Imvani mau anga, inu anthu anzeru, mutchere khutu, inu odziŵa zinthunu.
3
Pakuti khutu limamvetsa mau monga momwe m'kamwa mulaŵira chakudya.
4
Tiyeni tisankhe zolungama, titsimikize tokha zimene zili zabwino.
5
Pakuti aYobe anena kuti, ‘Ndine wosalakwa, koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.
6
Ngakhale ndine wolungama, akundiyesa wabodza. Mavuto anga ndi osatha, ngakhale ndine wosachimwa.’
7
Kodi pali munthu amene angafanefane ndi aYobe? Iwoŵa apambana kunyoza Mulungu.
8
Amayenda ndi anthu ochita zoipa, amayanjana ndi anthu a mtima woipa.
9
Paja ankanena kuti, ‘Palibe phindu kuti munthu azikondwerera Mulungu.’
10
“Tsono mumve, inu anthu anzerunu, Mulungu sangathe kuchita choipa, Mphambe sangathe kulakwa mpang'ono pomwe.
11
Amambwezera munthu potsata ntchito zake, munthuyo zinthu zimamgwera malinga ndi mayendedwe ake.
12
Ndithudi, Mulungu sangachite choipa, Mphambe sangaweruze mosalungama.
13
Kodi ndani adampatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi? Ndani adaika dziko lapansi m'manja mwake?
14
Iye akadalanda moyo wake, akadamulamula kuti mpweya wake ubwerere kwa Iye mwini,
15
bwenzi zamoyo zonse zitaonongeka, bwenzi anthu onse atabwerera ku fumbi.
16
“Ngati ndinu omvetsa, mumve zimenezi, mumvetsere bwino zimene ndikunenazi.
17
Kodi munthu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira? Kodi mungathe kumuweruza Mulungu Wolungama ndi Wamphamvu uja kuti ndi wolakwa?
18
Mulungu amadzudzula mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’ amauza akalonga kuti, ‘Ndinu oipa.’
19
Iye sachita zokondera kwa akuluakulu, kapena kulemekeza olemera kupambana osauka, pakuti onsewo Mulungu adaŵalenga ndi manja ake.
20
Iwowo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku Mulungu amakantha anthu, iwowo nkufa, anthu amphamvu amaŵalanda moyo mosavuta.
21
“Mulungu amapenya njira zonse za anthu, amaona mayendedwe ao onse.
22
Palibe usiku kapena mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoipa angathe kubisalira Mulungu.
23
Mulungu sasoŵa kuchita kumuikira munthu wina aliyense nthaŵi yoti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.
24
Iye amatsitsa atsogoleri, mlandu wao osaufufuza nkomwe, ndipo m'malo mwao amaikamo ena.
25
Iyeyo amadziŵa bwino ntchito zao, amaŵagubudula usiku, iwowo nkutswanyika.
26
Amaŵakantha chifukwa cha kuipa kwao, anthu ena onse akupenya,
27
chifukwa adapatuka osamtsata, ndipo sankasamala malamulo ake.
28
Adaliritsa amphaŵi kuti afuule kwa Mulungu, ndipo Iyeyo adamva kufuula kwa ovutikawo.
29
Kodi Mulungu akangoti duu, ndani anganene kuti walakwa? Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumpenyabe. Komabe ndiye amene amasamalira munthu kapena mtundu wa anthu,
30
kuti asalamulidwe ndi anthu osadziŵa Mulungu, ndipo asakodwe m'misampha yao.
31
“Kodi alipo amene adauza Mulungu kuti, ‘Ndalangika, sindidzachimwanso,
32
mundiphunzitse zimene sindikuziwona: ngati ndidachita choipa, sindidzachitanso’?
33
Kodi Mulungu akuweruzeni potsata m'mene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Inu ndinu amene muyenera kusankha osati ine. Nchifukwa chake munene zimene mukudziŵa.
34
Anthu omvetsa zinthu adzandikambira, anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,
35
‘Yobe akulankhula mosadziŵa, mau ake ndi opanda nzeru.’
36
Kunali bwino aYobe akadayesedwa mpaka ku mapeto, chifukwa choti amayankha monga m'mene amayankhira anthu oipa.
37
Pa tchimo lao aonjezerapo upandu, akunyadira zochita zao, ndipo akuchulukitsa mau onyoza Mulungu ife tilikumva.” Mulungu amasamalira zochitika pa dziko lapansi.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42