bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 39
Job 39
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 40 →
1
“Kodi iwe umaidziŵa nthaŵi imene zinkhoma zimaswera? Kodi udaziwonapo nswala zikubadwa?
2
Kodi ungathe kuŵerenga miyezi imene zimakhala ndi bele? Kodi nthaŵi imene nyamazi zimaswa iwe umaidziŵa?
3
Kodi ukuidziŵa nthaŵi imene zidzakhala tsonga nkuswa ana, kenaka nkutayiza?
4
Ana a nyamazi amakhala amphamvu, namakulira ku thengo. Pambuyo pake amapita, osabwereranso kwa mai wao.
5
“Kodi abulu akuthengo adaŵapatsa ndani ufulu wongodziyendera? Ndani adaŵapatsa liŵilo lao?
6
Ine ndidaŵapatsa chipululu kuti chikhale malo ao okhalako, ndiponso chichere kuti chikhale dera lao.
7
Amakhala kutali ndi mizinda yaphokoso, ndipo sadziŵa mau okuwa a anthu oyendetsa nyama zakatundu.
8
Kumapiri ndiko kumene kuli busa lao. Kumene amafunafuna msipu woti adye.
9
“Kodi njati ingavomere kukutumikira? Kodi ingagone m'khola mwako usiku?
10
Kodi ungathe kuimanga ndi nsinga kuti izilima? Kodi ingasalaze nthumbira m'munda mwako?
11
Kodi ungadalire njatiyo chifukwa cha mphamvu zake? Kodi ungayembekeze kuti ikugwirira ntchito yako?
12
Kodi ungakhulupirire kuti idzabwera nkudzatuta tirigu wako ku malo opunthira?
13
“Nthiŵatiŵa ikukupiza mapiko ake monyadira, koma nthenga zake ndi mapiko ake sizikuithandiza kuuluka monga amachitira kakoŵa.
14
Nthiŵatiŵa imafotsera mazira ake pansi, kuti afundidwe m'nthaka.
15
Koma imaiŵala kuti mapazi ake omwe angathe kuphwanya mazirawo, ndipo kuti nyama zakuthengo nkuŵapondereza.
16
Nthiŵatiŵa imachita ana ake nkhalwe ngati si ake. Zakuti idaavutika poŵabereka imaiŵalako.
17
Paja Mulungu adaimana nzeru, kotero kuti simvetsa kanthu kalikonse.
18
Komabe nthiŵatiŵayo ikadzambatuka nkuyamba kuthaŵa, imamsiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.
19
“Kodi ndiwe amene umapatsa mphamvu kavalo? Nanga ndiwe amene umaveka chenjerere m'khosi mwake?
20
Kodi ndiwe amene umamlumphitsa ngati dzombe? Kavalo akamadzuma, mpweya wake ndi waukali ndiponso woopsa.
21
Kavaloyo amalumphalumpha m'chigwa, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.
22
Sachita mantha, sachita nkhaŵa, ndipo sabwerera m'mbuyo akaona lupanga.
23
Zida zankhondo za wokwerapo wake zimachita kwichikwichi m'phodo, ndipo mkondo ndi nthungo zimanyezemira pa dzuŵa.
24
Akavalowo amanjenjemera ndi ukali nathamangira kutsogolo, ndipo akangomva lipenga sangathe kuima.
25
Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali. Amamva kufuula kwa atsogoleri ankhondo.
26
“Kodi ndi nzeru zako zimene zimaphunzitsa kabaŵi kuuluka, ndi kutambalitsa mapiko ake kupita chakumwera?
27
Kodi umalamula chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka? Kodi udachiphunzitsa ndiwe kukamanga chisa pamwamba penipeni?
28
Chimakhala pa phiri, nkumanga chisa chake pamenepo, pansonga penipeni pa thanthwe losakwereka.
29
Pamenepo chimayang'ana choti chigwire kuti chidye, ndipo maso ake amachiwonera patali chinthucho.
30
Ana ake amayamwa magazi, amapezeka kumene kuli mitembo.” Kuyankha kwa Yobe.
← Chapter 38
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 40 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42