bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 5
Job 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 6 →
1
“Iwe Yobe, itana tsono. Kodi alipo wina aliyense adzakuyankhe? Kodi ndi kwa mngelo uti ungapeze thandizo?
2
Pajatu mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru zimaononga wopusa.
3
Ine ndidaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake ndidaitemberera.
4
Ana ake alibe nchitetezo chomwe, amaŵapondereza m'bwalo lamilandu, palibe wina aliyense woŵapulumutsa.
5
Anthu anjala amamdyera zokolola zake, amamtengera ndi zapaminga zomwe. Anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.
6
Masautso satuluka m'fumbi, ndipo zovuta sizichokera m'dothi ai.
7
Koma chibadwire munthu amangodzitengera mavuto yekha mosalephera, monga momwe sizilepherera mbaliwali kuulukira ku mlengalenga, kuchokera pa moto.
8
“Achikhala ndinali ine, ndikadatembenukira kwa Mulungu, ndikadapereka mlandu wanga kwa Iye.
9
Ntchito zake ndi zazikulu ndi zosamvetseka. Zodabwitsa zimene amachita ndi zosaŵerengeka.
10
Amagwetsa mvula pa dziko lapansi, ndipo amathirira minda ya anthu.
11
Amakweza anthu oluluka, ndipo amasangalatsa anthu olira.
12
Amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chao sichiphula kanthu.
13
Amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwao, amathetsa msanga zimene akapsala adakonza kuti achite.
14
Iwowo amakumana ndi mdima ngakhale masana, amayambasa masanasana ngati usiku.
15
Koma Mulungu amateteza amphaŵi kwa adani oŵasinjirira, amapulumutsa osauka kwa anthu ofuna kuŵapanikiza.
16
Choncho amphaŵi amaŵalimbitsa mtima, koma anthu oipa amaŵatseka pakamwa.
17
“Ndi wodala munthu amene Mulungu amamdzudzula. Nchifukwa chake usamanyoze chilango cha Mphambe.
18
Pakuti ndiye amene amavulaza namangaponso mabala. Amakantha, komanso manja ake amachiritsa.
19
Iye adzakupulumutsa ku masautso nthaŵi ndi nthaŵi. Zovuta sizidzakukhudza konse, zingachuluke bwanji.
20
Pa nthaŵi ya njala adzakusamala, pa nthaŵi ya nkhondo adzakupulumutsa.
21
Adzakuteteza kwa anthu osinjirira, chiwonongeko chikadzafika, sudzachiwopa.
22
Pa nthaŵi ya chiwonongeko ndi ya njala uzidzaseka, zilombo zakuthengo sudzaziwopa.
23
M'minda mwako simudzakhala miyala, nyama zakuthengo sizizakuvuta.
24
Udzadziŵa kuti nyumba yako ndi malo amtendere, udzaona kuti pa zoŵeta zako palibe chosoŵa.
25
Udzadziŵa kuti ana ako adzakhala ambiri, ndipo kuti zidzukulu zako zidzachuluka ngati udzu.
26
Udzafika ku manda utakalamba, monga m'mene zokolola zimachera pa nyengo yake.
27
Iwe Yobe, zonsezi ife tazifufuzafufuza, ndipo taona kuti ndi zoona. Uzimvere ndi kuzitsata zimenezi.”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42