bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 31
Job 31
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 32 →
1
“Ndidalonjezana ndi maso anga, ndikadatha bwanji kupenyetsetsa namwali?
2
Kodi Mulungu kumwamba akadandisungira zotani? Kodi Mphambe kumwamba akadandikonzera zabwino zanji?
3
Wosalungama tsoka limamgwera, wochita zoipa amaonongeka.
4
Koma Mulungu amaona zochita zanga, amadziŵa mayendedwe anga onse.
5
“Sindidachite zachiphamaso, sindidayesepo kunyenga anthu.
6
Mulungu andiyese pa sikelo ya chilungamo, adziŵe kuti ndine wangwiro.
7
Ngati mayendedwe anga asempha njira, ngati mtima wanga wakhumbira zinthu molakwa, ndipo ngati ndachita choipa chilichonse,
8
pamenepo zimene ine ndidabzala adye ndi ena, zomera zanga zizulidwe.
9
“Ngati mtima wanga udanyengedwapo ndi mkazi, ndipo ngati ndidalalira pa khomo la mnansi wanga,
10
pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya, ndipo azigona naye.
11
Pakuti limenelo likadakhala tchimo loopsa zedi, ukadakhala mlandu umene oweruza amaperekapo chilango chachikulu.
12
Kuipa kwake kukadakhala ngati moto woonongeratu, ukadapsereza zinthu zanga zonse.
13
“Ngati ndidapondereza mlandu wa mtumiki wanga, wamwamuna kapena wamkazi, pamene adabwera kwa ine ndi madandaulo ake,
14
ndidzatani ine pamene Mulungu adzadzambatuke? Nanga akadzandifunsa, ndidzayankha chiyani?
15
Kodi amene adapanga ine m'mimba mwa amai anga si yemwe adapanganso iyeyo? Kodi si mmodzi yemweyo amene adatilenga tonsefe?
16
“Ngati amphaŵi ndidaŵamana zimene ankakhumba, kapena kuŵagwiritsa mwala mwankhanza akazi amasiye,
17
ngati chakudya ndidadya ndekha, ana amasiye osachilaŵa,
18
pakuti anawo ndidaŵalera ngati bambo wao ndi kuŵasamalira bwino chibadwire chao,
19
ngati ndidaona wina aliyense akuzunzika ndi usiŵa, kapena munthu wosauka alibe chofunda,
20
ngati iyeyo sadanditamande chifukwa chomupatsa chovala, ndipo ngati sindidamfunditsa ndi nsalu za ubweya wa nkhosa,
21
ngati ndidaopsezapo mwana wamasiye, podziŵa kuti ku bwalo lamilandu sadzanditsutsa,
22
pamenepo phewa langa lipokonyoke, mkono wanga ukonyoke m'maluma mwake.
23
Pakutitu tsoka lochokera kwa Mulungu ndimachita nalo mantha, sindikadatha kuchita kanthu kalikonse koipa pamaso pake.
24
“Sindidaike mtima pa chuma, kapena kudalira golide wabwino kwambiri.
25
Zedi, sindidakondwere chifukwa choti chuma changa chinali chambiri, kapena chifukwa choti manja anga adapata zambiri.
26
Poona dzuŵa likuŵala, kapena mwezi ukuwonetsa kukongola kwake,
27
mtima wanga ukadakopeka nazo, dzanja langa nkuliika pakamwa mozilemekeza,
28
bwenzi limeneli lili tchimo loti aweruzi andilange nalo, chifukwa ndikadakhala wonama kwa Mulungu wakumwamba.
29
“Sindidakondwerere kuwonongeka kwa mdani wanga. Sindidasekere tsoka litamgwera.
30
Sindidachimwe ndi pakamwa panga, potemberera mdani wanga kuti aonongeke.
31
Amene ndimakhala nawo amadziŵa kuti ine ndimalandira alendo ndi kuŵapatsa chakudya chokwanira.
32
Alendo sindidaŵasiye panja m'miseu. Aliyense wofika pakhomo panga ndidampatsa malo ogona.
33
Anthu ena amabisa zoipa zao, koma ine sindidabise cholakwa chilichonse.
34
Sindidaope zokambakamba za anthu kapena zonyoza za banja lina lililonse, sindidakhale chete kapena kubindikira m'nyumba chifukwa choopa iwowo.
35
“Ha, pakadakhala wina wondimva! Ndikulumbira kuti ndikulankhula zoona. Mphambe andiyankhe. Mdani wanga akadachita kulemba pa kalata mau ake ondineneza,
36
ndikadachita kuipachika kalatayo paphewa panga monyadira, ndikadaivalanso kumutu ngati chisoti chaufumu.
37
Ndikadamsimbira Mulungu zonse zimene ndachita, ndikadafika pamaso pake ngati kalonga.
38
“Ngati ndidalanda minda ya anthu ena osagula, ngati ndikulima pa minda ya eniake,
39
ngati ndidadya zam'minda osagula, ngati ndidaphetsa eni mindayo,
40
m'mindamo mumere minga m'malo mwa tirigu mumere namsongole m'malo mwa barele.” Mau a Yobe athera pano. Elihu adzudzula Yobe ndi abwenzi aja.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42