bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 16
Job 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 17 →
1
Yobe adayankha kuti,
2
“Zoterezi ndidazimva kale. Nonsenu ndinu anthu osatha kuthuzitsa mtima mnzanu.
3
Kodi mudzakhala mukulankhulabe mau achabechabeŵa mpaka liti? Kaya chakuvutani nchiyani kuti muzilankhulabe mau otsutsaŵa?
4
Inenso ndikadalankhula monga inu, mukadakhala monga ndiliri inemu. Inenso ndikadatha kulankhula monga mukulankhuliramu. Nanenso ndikadakupukusirani mutu.
5
Ndikadakulimbitsani ndi mau anga, ndikadakuthuzitsani mtima ndi kuchepetsa zoŵaŵa zanu.
6
“Ine ndikati ndilankhule, zoŵaŵa zanga sizichepa. Ndikati ndikhale chete, zoŵaŵazo zikhala zilipobe.
7
Ndithudi, Mulungu wanditha mphamvu, waononga banja langa lonse.
8
Wandigwira, ndipo wasanduka mdani wanga, umboni woti ndine wolakwa. Ndatsala mafupa okhaokha, ndipo chimenechi chikunditsimikiza kuti ndine wolakwa.
9
Mulungu wanding'amba ali chikwiyire, ndipo akudana nane, wachita kulumira mano. Mdani wanga akundituzulira maso.
10
Anthu amandinyoza polankhula, amandimenya pa tsaya mwachipongwe, akundichitira upo kuti alimbane nane.
11
Mulungu wandipereka kwa anthu osasamala za Iye, wandiponya m'manja mwa anthu oipa.
12
Ndidaali pa mtendere, koma Mulungu adanditswanya. Adandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Adandiimika kuti ndikhale choponyerapo chandamale chake.
13
Mivi yake ikundilasa pa mbali zonse. Walasa impso zanga mopanda chifundo, watayira pansi ndulu yanga.
14
Akundivulazavulaza. Akulimbana nane ngati munthu wankhondo.
15
“Ndasokerera chiguduli pathupi panga. Ndaika mphamvu zanga pa fumbi.
16
Maso anga afiira nkulira, ndipo zikope zanga zatupa kwambiri.
17
Koma sindidachite chiwawa chilichonse, pemphero langa kwa Mulungu ndi lolungama.
18
“Iwe, dziko lapansi, usabise zoipa zimene andichita. Kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke.
19
Tsopano lino mboni yanga ili kumwamba, wonditchinjiriza ali komweko.
20
Abwenzi anga akundinyodola, choncho ndikulirira kwa Mulungu.
21
Kukadapezeka wondipepesera kwa Mulungu, bwenzi atandipepesera, monga momwe munthu amachitira mnzake.
22
Pakuti zitapita zaka pang'ono, ndidzayenda njira imene sindidzabwerera.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42