bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 20
Job 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 21 →
1
Zofari wa ku Naama adayankha kuti,
2
“Iwe Yobe, wandipsetsa mtima. Nchifukwa chake ndikufulumira kuyankha.
3
Ndikumva mau ondidzudzula ndi ondinyoza, koma ndadziŵa kale m'mene ndingathe kuyankhira.
4
Kodi sukudziŵa zimene zidachitika masiku amakedzana, kuyambira nthaŵi imene munthu adalengedwa pa dziko.
5
Kodi sukudziŵa kuti kukondwera kwa woipa nkosakhalira kutha? Kodi sukudziŵa kuti chimwemwe cha munthu wopanda Mulungu ncha kanthaŵi chabe?
6
Ngakhale mbiri yake ifalikire ponseponse, ndipo ulemerero wake ukwere kufikira ku mlengalenga,
7
adzatheratu monga momwe imatayikira ndoŵe yake. Amene ankamuwona azidzafunsa kuti, ‘Kodi uje uja ali kuti?’
8
Adzangozimirira ngati maloto, ndipo sadzapezekanso. Adzachotsedwa ngati zinthu zoonekera anthu kutulo usiku.
9
Amene adamuwona kale sadzamuwonanso, sadzapezekanso kunyumba kwake.
10
Ana ake adzabwezera zonse, zimene iyeyo adalanda anthu osauka.
11
Thupi lake ndi la nyonga zaunyamata, komabe nyongazo zidzatha naye limodzi m'fumbi.
12
“Zoipa zimakhala zozuna kwa iye, nchifukwa chake amachita ngati kuzisunga m'kamwa mwake.
13
Ngakhale safuna kuleka kuzivumata, nangozisunga m'kamwa mwakemo,
14
zoipazo akazimeza, zimaloŵa m'mimba mwake. Zimasanduka ngati ndulu ya mphiri m'kati mwa iyeyo.
15
Amapeza chuma, koma amachisanzanso. Mulungu amachitulutsa m'mimba mwa munthuyo.
16
Zimene amadya zili ngati ululu wa mphiri, ndipo ululuwo udzamupha.
17
Sadzaona mitsinje ya mafuta a olivi, kapena mifuleni ya madalitso a m'dziko lamwanaalirenji.
18
Adzabweza zimene adapata pogwira ntchito. Sadzadyerera chuma chake. Sadzapeza mpata wokondwerera phindu la malonda ake.
19
Pakuti adapondereza amphaŵi ndi kuŵasiya osaŵasamala, ndipo adalanda nyumba zimene sadamange ndiye.
20
“Chifukwa choti umbombo wake unali wosakata, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho.
21
Iyeyo ankati akadya, ankadyeratu zonse, tsono chuma chake chidatheratu.
22
Ngakhale ndi wachuma, adzakhala mmphaŵi. Mavuto aakulu adzamgwera.
23
Pa nthaŵi yoti adyerere chuma china, Mulungu adzamgwetsera ukali wamoto ngati mvula yosakata.
24
Adzathaŵa mkondo wachitsulo, koma adzalasidwa chipyoza ndi muvi wamkuŵa.
25
Muviwo atautulutsa m'thupi mwake, atachotsa nsonga yake yonyezemira yobaya ndulu yake, iyeyo adzagwidwa ndi mantha aakulu.
26
Zonse zimene adazipeza, zazimirira ngati mu mdima. Moto wopanda woukwereza wamupsereza, watentha iyeyo pamodzi ndi zonse zotsalira m'nyumba mwake.
27
Zamumlengalenga zidzaulula zolakwa zake, za pansi pano zidzamuukira.
28
Chigumula cha madzi chidzaononga nyumba yake. Katundu wake yense adzachotsedwa pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu.
29
Izi nzimene Mulungu amasungira munthu woipa. Ndizo zimene Mulungu adalamula kuti zikhale mphotho ya munthuyo.” Yobe
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42