bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 15
Job 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 16 →
1
Apo Elifazi wa ku Temani adayankha kuti,
2
“Kodi munthu wanzeru angalankhule zachabechabe motere? Kodi angathe kutulutsa mau opandapake ongouluka ngati mphepo?
3
Kodi angathe kulankhula zinthu zopandapake, kapena kunena mau opanda phindu?
4
Koma iwe ukufuna kuti anthu asamaope Mulungu, ukufuna kuti aleke kusinkhasinkha za Mulungu.
5
Tchimo lako likuwonekera ndi kalankhulidwe kako, koma umafuna kudzilungamitsa ndi kuchenjera pakamwa kwako.
6
Choncho ndi mau ako omwe amene akukutsutsa, osati ine. Pakamwa pako pomwe pakuchita umboni wokuzenga mlandu.
7
“Kodi munthu woyamba kubadwa ndiwe? Kodi udaalipo pamene Mulungu ankalenga mapiri?
8
Kodi uli m'gulu la alangizi a Mulungu? Kodi ukuyesa wanzeru ndiwe wekha?
9
Kodi nchiyani chimene umadziŵa iwe, chosachidziŵa ife? Kodi chilipo chimene umamvetsa iwe, chosachimvetsa ife?
10
Pakati pa ife pano tili ndi anthu aimvi ndi okalamba, amvulazakaletu kupambana bambo wako.
11
Kodi akukuchepera mau othuzitsa mtima ochokera kwa Mulunguŵa, kapena mau okulankhula mofatsaŵa?
12
“Nanga chifukwa chiyani ukupsa mtima? Chifukwa chiyani ukutituzulira maso?
13
Chifukwa chiyani ukufuna kulimbana ndi Mulungu? Chifukwa chiyani ukumnyoza ndi pakamwa pako?
14
Kodi munthu nchiyani kuti angathe kukhala wosachimwa? Kapena wobadwa kwa mkazi nchiyani, kuti angakhale wopanda uchimo pamaso pa Mulungu?
15
Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake. Ngakhale akumwamba omwe sali angwiro pamaso pake.
16
Nanji tsono munthu, amene ali wonyansa ndi wachabechabe, amene kuchita zoipa kuli ngati kumwa madzi!
17
“Undimve, ine ndikufotokozera, zimene ndidazimva ndikuuza.
18
Zoonazo adandiphunzitsa ndi anthu anzeru, sadandibisire zimene adamva kwa makolo ao.
19
Dziko lao linali lopanda anthu achilendo, amene adakaŵachotsa mu njira yake ya Mulungu.
20
Munthu woipa amakhala akuvimvinika ndi zoŵaŵa masiku onse a moyo wake. Munthu wankhalwenso adzavutika zaka zake zonse.
21
Amamva mau oopsa m'makutu mwake, pamene akuyesa kuti ali pabwino, achifwamba adzamthira nkhondo.
22
Sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa, akuyenera kuphedwa ndithu basi.
23
Amangoyendayenda paliponse, kunka nafuna chakudya nkumati, ‘Kodi chili kuti?’ Amadziŵa kuti tsiku lamdima lili pafupi.
24
Masautso ndi nthumanzi zimamchititsa mantha kwambiri. Zimenezi zimamgudukira koopsa, monga imachitira mfumu imene yakonzekera kukamenya nkhondo.
25
Zonsezi zamugwera chifukwa adaukira Mulungu. Adafuna kulimbana ndi Mphambe.
26
Adatenga chishango chake mwaliwuma, ndipo adathamanga kuti akalimbane ndi Mulungu.
27
“Ngakhale nkhope yake ndi yokulupala, ngakhale m'chiwuno mwake muli monenepa kwambiri,
28
munthuyo adzasauka m'mizinda yoonongeka. Adzakhala m'nyumba zosayenera kukhalamo anthu, chifukwa zidaonongeka pa nkhondo.
29
Iyeyo sadzalemera, chuma chake sichidzakhalitsa. Minda yake sidzaberekanso pa dziko lapansi.
30
Iyeyo sadzatuluka m'mavuto, adzakhala ngati mtengo umene nthambi zake zapsa ndi moto, Umene maluŵa ake adzachotsedwa ndi mpweya wa Mulungu.
31
Asadzinyenge pokhulupirira zinthu zoipa zachabe, poti zinthu zachabezo ndizo zidzakhale malipiro ake.
32
Adzafota nthaŵi isanakwane, ndipo nthambi yake sidzaphukanso.
33
Adzakhala ngati mtengo wamphesa umene umayoyola zipatso zake zisanapse. Adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluŵa ake.
34
Anthu osamvera Mulungu adzakhala opanda zidzukulu. Olandira ziphuphu moto udzapsereza nyumba yao.
35
Ameneŵa ndiwo amalingalira zaupandu namachita zoipa. Mtima wao umaganizira zonyenga nthaŵi zonse.”
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42