bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 36
Job 36
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 37 →
1
Ndipo Elihu adapitirira kulankhula, nati:
2
“Mundilole pang'ono, ndipo ndikuphunzitsani. Pakuti zilipobe zoti ndinene m'malo mwa Mulungu.
3
Nzeru zanga zikhala zochokera patali, ndiwonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.
4
Ndithudi, sindikunena zabodza. Wolankhula nanune ndine wanzeru kotheratu.
5
“Zoonadi, Mulungu ndi wamphamvu, sanyoza munthu aliyense, ndipo amadziŵa zonse.
6
Salola oipa kuti akhalebe ndi moyo, koma anthu osauka amaŵachitira zolungama.
7
Iyeyo amatchinjiriza anthu opanda chifukwa, amalola kuti alamulire ngati mafumu, ndipo motero amalemekezeka mpaka muyaya.
8
Koma anthu akamangidwa ndi nsinga, namazunzika chifukwa cha zimene adachita,
9
pamenepo Mulungu amaŵasonyeza ntchito zao ndi zolakwa zao, kutsutsa kudzikuza kwao kochita kunyanya.
10
Amaŵatsekula makutu kuti amve malangizo ake, amaŵalamula kuti asiye zoipa.
11
Ngati anthu amumvera ndi kumamtumikira, adzatsiriza masiku a moyo wao mwamtendere, adzatsiriza zaka zao mosangalala.
12
Koma akapanda kumvera, adzaonongeka ndi lupanga, adzafa osadziŵa kanthu.
13
“Anthu onyoza Mulungu mumtima mwao amaputa mkwiyo wake, Mulungu akaŵalanga, iwo safuula kupempha chithandizo.
14
Amafa akali biriŵiri, ndipo moyo wao umathera m'zonyansa.
15
Koma Mulungu amapulumutsa ovutika mwa njira ya mazunzo ao omwe, amaŵatsekula makutu poŵagwetsa m'mavuto.
16
Inuyo Mulungu adakutulutsaninso m'mavutowo, afuna kukuikani pabwino, osasoŵa kanthu kalikonse.
17
“Koma tsopano inu mwapezeka opalamula ngati anthu oipa, choncho chilango cholungama cha Mulungu chakugwerani.
18
Muchenjere kuti chuma chingakuphimbeni m'maso, musalole kuti chiphuphu chikusokezeni.
19
Kodi kulira kwanu kungakuchotseni m'mavuto? Kodi mphamvu zanu zingakupulumutseni?
20
Musalakelake kuti usiku ubwere, chifukwa ndiyo nthaŵi imene mitundu ya anthu idzaonongeka.
21
Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo, chifukwa uchimowu ndiwo udadzetsa kuzunzika kwanu.
22
Zoonadi, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?
23
Palibe ndi mmodzi yemwe angauze Mulungu zoti achite. Palibe aliyense amene anganene kuti ‘Mulungu ndi wolakwa.’
24
“Kumbukirani kutamanda ntchito za Mulungu, zimene anthu amaziyamika ndi nyimbo.
25
Anthu onse amaona ntchitozo, koma palibe wozindikira m'mene ziliri.
26
Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu kwambiri, sitimdziŵa mpang'ono pomwe. Chiŵerengero cha zaka zake nchosadziŵika.
27
Mulungu ndiye amakweza timadontho ta madzi ku thambo kuchokera pansi, ndipo amasungunula mitambo kuti ikhale mvula.
28
Mitambo imatsanyula mvulayo, ndipo mvulayo imavumba pa anthu mokwanira.
29
Kodi alipo wina woti angadziŵe kuyenda kwa mitambo kapena kugunda kwa zing'aning'ani?
30
Mulungu amaŵalitsa zing'aning'ani kuthambo kwake konse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja.
31
Mulungu amachenjeza mitundu ya anthu podzera m'zimenezi, komabe amapereka chakudya chochuluka.
32
Amagwira zing'aning'ani, ndipo amazilamula kuti zigwe pa malo amene Iye akufuna.
33
Kugunda kwake kumalengeza kuti Iye alipo, ndiye amalanga uchimo mwaukali.
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 37 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42