bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 41
Job 41
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 42 →
1
Kodi ungathe kuchikoka ndi mbedza ya nsomba chilombo chija cha Leviyatani, kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
2
Kodi ungathe kuchimanga chingwe m'mphuno mwake, kapena kuchiboola nsagwada ndi mbedza?
3
Kodi chidzakupempha kuti uchimasule? Kodi chidzakupemba kuti uchichitire chifundo?
4
Kodi chidzachita nawe chipangano kuti chikhale chokutumikira mpaka muyaya?
5
Kodi ungaseŵere nacho ngati mbalame? Kodi kapena nkuchimanga ndi unyolo kuti adzakazi ako aseŵere nacho?
6
Kodi asodzi nkuchitsatsa malonda? Nanga amalondawo nkugaŵanagaŵana nyama yake kuti akaigulitse?
7
Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi ntcheto, kapena kuboola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
8
Ukachiputa, udziŵe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso.
9
Ndithu, aliyense akachiwona chilombocho, amataya mtima, ndipo amangodzigwera ndi mantha.
10
Ngati palibe wina woti angalimbe mtima nkuchiputa. Nanga ndani angalimbe mtima nkukangana ndi Ine Mulungu?
11
Kodi ndani adandipatsa kanthu, kuti Ineyo ndimbwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.
12
“Sindingaleke kulankhula za ziwalo zake za chilombocho, za mphamvu zake ngakhalenso za maonekedwe a thupi lake.
13
Ndani angasende chikopa chake? Ndani angachibaye chikopa chimene chija, kulimba konse kuja ngati chovala chachitsulo?
14
Ndani angatsekule kukamwa kwake? Mano ake ndi oopsa.
15
Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana, onse olimba ngati mwala.
16
Mambawo ndi olukanalukana, kotero kuti ndi mpweya womwe sungathe kuloŵa pakati pake.
17
Ndi olumikizanalumikizana, ndi omamatirana kwambiri, kotero kuti sangathe kutayana.
18
Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali, maso ake amaŵala ngati kuŵala kwa mbandakucha.
19
M'kamwa mwake mumatuluka nsakali za moto, mumathetheka mbaliwali za moto.
20
M'mphuno mwake mumatuluka utsi, ngati wa m'nkhali yogaduka ndiponso ngati wa moto wa mlulu.
21
Mpweya wake umayatsa makala, malaŵi a moto amatuluka m'kamwa mwake.
22
Khosi lake ndi lamphamvu kwambiri, aliyense wokumana nacho amangoti njenjenje ndi mantha.
23
Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana, ndi yokhwima kwambiri, ndipo ndi yolimba.
24
Pachifuwa pake mpouma ngati mwala. Pali gwa! Ngati mwala wa mphero.
25
Chilombocho chikangoti vuuku, ndi amphamvu omwe amaopa. Akamva phokoso lake, amachita mantha.
26
Ngakhale lupanga lichikanthe, silichichita kanthu. Mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.
27
Chitsulo chimachiyesa phesi chabe, mkuŵa chimauyesa chikuni choola.
28
Muvi sungathe kuchithaŵitsa, Miyala imene achilasa nayo, chimangoinyenyanyenya.
29
Zibonga zimakhala ngati ziputu. Akamachitchaya ndi nthungo, icho chimangoseka.
30
Za kumimba kwake zili ngati mapale akuthwa. Chimatambalala m'matope ngati galeta lopunthira tirigu.
31
Chimagadutsa madzi ozama ngati madzi am'nkhali, chimasandutsa nyanja kuti igaduke ngati mbiya yoyengeramo mafuta.
32
Kumbuyo kwake chimasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.
33
Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, ncholengedwa chopanda mantha.
34
Chimanyoza nyama zina zonse. Icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.” Mau omaliza a Yobe.
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 42 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42