bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 2
Job 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 3 →
1
Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi.
2
Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikuyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.”
3
Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wazindikirapo mtumiki wanga Yobe, kuti safanafana ndi wina aliyense pa dziko lapansi? Iye uja ndi munthu wosalakwa ndi wolungama. Amandimvera Ine Mulungu, ndipo amapewa zoipa. Iyeyo akali ndithu wokhulupirikabe kwambiri, ngakhale kuti iwe paja udaandiwumiriza kuti ndikulole kuti umuvutitse popanda chifukwa.”
4
Apo Satana adayankha kuti, “Koma ayesedwe m'thupi mwake. Zinthu zonse zimene munthu ali nazo angathe kuzipereka, chikulu iyeyo ali moyo.
5
Koma tsopano taonongani thupi lake, muwona, adzakutukwanirani pamaso.”
6
Chauta adauza Satana uja kuti, “Chabwino, iyeyo uchite naye zonse zimene ukufuna, koma moyo wake wokha usauchotse.”
7
Choncho Satana adachoka kumsiya Chauta napita kukazunza Yobe ndi zilonda zoopsa pa thupi lonse.
8
Pamenepo Yobe adatenga phale kuti azidzikandira, nakakhala pa dzala.
9
Tsono mkazi wake adamuuza kuti, “Ha! Mukukhalabe okhulupirika motere! Ingomtukwanani Mulunguyo, mufe basi!”
10
Koma Yobe adauza mkazi wakeyo kuti, “Ukulankhula ngati mkazi wopusa. Ngati tilandira zokondweretsa kwa Mulungu, tilekerenji kulandiranso zoŵaŵa?” Motero pa zonsezi Yobe sadachimwe polankhula pake.
11
Tsono abwenzi ake a Yobe, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki, ndi Zofari wa ku Naama, adazimva za masoka onseŵa amene adamgwera. Ndiye tsiku lina anthu atatuwo adabwera, aliyense kuchokera kwao. Onsewo anali atapangana za nthaŵi yoti adzampepese ndi kudzamsangulutsa.
12
Ataona Yobeyo chakutali, sadamzindikire, ndipo adayamba kulira mofuula. Adang'amba zovala zao, nadzithira fumbi kumutu.
13
Adakhala ndi Yobeyo masiku asanu ndi aŵiri, usana ndi usiku womwe. Koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene ankalankhula naye, chifukwa chozindikira kuti Yobeyo akuvutika kwambiri.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42