bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 14
Job 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 15 →
1
“Munthu wobadwa mwa mkazi amakhala masiku oŵerengeka, komanso masiku ake ndi amavuto okhaokha.
2
Amaphuka ngati duŵa, kenaka nkufota. Sakhalitsa, amathaŵa ngati mthunzi.
3
Kodi Inu Mulungu, mungamtuzulire maso woteroyo? Kodi mungamzenge mlandu?
4
Ndani angatulutse chabwino m'choipa? Palibe ndi mmodzi yemwe.
5
Masiku a munthu ndi oŵerengeka, chiŵerengero cha miyezi yake mumachidziŵa ndinu. Inu mudamulembera malire ake, sangathe kuŵalumpha.
6
Mumleke tsono kuti apumule, akondweko, akondwerere moyo wake monga amachitira waganyu poweruka.
7
“Mtengo chiyembekezo chake nchakuti akaudula udzaphukanso, nthambi zake sizidzaleka kuphuka.
8
Ngakhale mizu yake ikalambe m'nthaka, ndipo chitsa chake chiwole,
9
komabe chinyontho chikafika, udzaphukira, udzaphukadi nthambi ngati mtengo wanthete.
10
Koma munthu akafa, kutha kwake nkomweko. Kodi munthuyo akafa, amapita kuti?
11
Monga madzi amaphwa m'nyanja, monganso mtsinje umaphwa nuuma,
12
momwemonso munthu amagona pansi osadzukanso. Mpaka zamumlengalenga zidzatha, iyeyo sadzadzuka. Palibe aliyense angamdzutse kutulo kwake.
13
Ha! Achikhala mudaangondibisa ku manda, kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita. Achikhala mudaangondiikira nthaŵi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso.
14
Kodi munthu atafa, nkudzakhalanso ndi moyo? Koma masiku onse a moyo wanga wovutikawu, ndidzadikira mpaka kumasulidwa kwanga kutafika.
15
Inu mudzandiitana, ine nkukuyankhani. Mudzafunitsitsanso kuwona ine, ntchito ya manja anune.
16
Nthaŵiyo mudzayang'ana mayendedwe anga onse, koma simudzalondoloza machimo anga.
17
Zolakwa zanga zidzakhululukidwa, Inu mudzafafaniza machimo anga onse.
18
“Komabe monga phiri limagwa nkuswekasweka, ndipo thanthwe limasendezeka kuchoka pamalo pake,
19
monganso madzi oyenda amaperesa miyala, ndipo madzi othamanga amakokolola nthaka, momwemonso Inu mumaononga chiyembekezo cha munthu.
20
Mumamtswanya munthu kamodzinkamodzi, iye nkufafanizika kotheratu. Mumasintha maonekedwe a nkhope yake, nkumtaya kutali.
21
Ana ake akamalemekezedwa, iye sadziŵako, akamachititsidwa manyazi, iye saziwona.
22
Amangomva zoŵaŵa za m'thupi mwake zokha, amangodzilira yekha mwiniwakeyo.” Elifazi
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42