bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 6
Job 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 7 →
1
Tsono Yobe adayankha kuti,
2
“Achikhala mavuto anga adaayesedwa, achikhala masoka anga adaaŵaika pa sikelo,
3
bwenzi atalemera kupambana mchenga wonse wam'nyanja. Nchifukwa chake kulankhula kwanga kuli kokadzulira.
4
Zoonadi mivi yake ya Mphambe yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo. Zoopsa za Mulungu zandizinga, kuti zilimbane nane.
5
Kodi bulu amalira akakhala ndi msipu? Nanga ng'ombe, kodi imalira ikakhala ndi chakudya?
6
Kodi chakudya nkuchidya chili zii, chopanda mchere? Kodi choyera cha dzira chimatsekemera?
7
Zakudya zimenezi sindifuna nkuzilaŵa komwe, zakudya zake ndi zobwerera kukhosi.
8
“Achikhala ndidaalandira chomwe ndikufuna, achikhala Mulungu adaandipatsa chimene ndikukhumba!
9
Achikhala kudaamkomera Mulungu kuti anditswanye, achikhala adaandimenya ndi dzanja lake, nkundiwonongeratu!
10
Zimenezi zikadandisangalatsa, ndikadakondwa nazo kwambiri ngakhale zipweteke chotani, podziŵa kuti sindidakane mau a Woyera uja.
11
Kodi mphamvu zanga ndi zotani kuti ndizikhalabe ndi moyo? Nanga moyo wanga ukupitiriranji, ngati chiyembekezo palibe?
12
Kodi ine ndidachita kuti gwa ngati mwala? Kodi thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo?
13
Zoona, ndilibenso mphamvu zodzipulumutsira, kulibenso kwina koti nkupezerako chithandizo.
14
“Pa mavuto ngati ameneŵa pafunika abwenzi okhulupirika, kuwopa kuti mwina mwake munthu angasiyane ndi Mphambe.
15
Koma abwenzi anga ndi onyenga, ngati mtsinje wothamanga, ngati mitsinje youma msanga mvula ikasoŵa.
16
Ali ngati mitsinje ya madzi abii nthaŵi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa cha kuchuluka kwa mvula.
17
Koma pa nthaŵi ya mafundi imauma, kukatentha imamwerera.
18
Anthu apaulendo amapatukirako kufuna madzi, koma amangoyendayenda nkufera m'chipululu.
19
Oyenda pa ngamira a ku Tema amaifunafuna mitsinjeyo. Alendo a ku Sheba amaidalira.
20
Amataya mtima chifukwa ankayembekeza kupeza madzi, koma pofika kumeneko, angoti kakasi, poti idauma.
21
“Tsono umu ndimo m'mene inuyo mwandichitira ine. Mwaona tsoka langa, ndipo mukuchita mantha.
22
Kodi ndanena kuti, ‘Mundipatse mphatso,’ kapena kuti, ‘Mupereke chiphuphu kwa wina chifukwa cha ine?’
23
Kodi ndanena kuti, ‘Mundipulumutse kwa mdani,’ kapena kuti, ‘Mundiwombole kwa ondizunza?’
24
“Chabwino, langizeni ndipo ndidzakhala chete. Dziŵitseni m'mene ndidachimwira.
25
Mau oona amalasa mtima, koma inu mukunditsutsa pa zotani?
26
Kodi inu mukufuna kundidzudzuliranji? Monga simukuwona kuti mau a munthu wotaya mtima ndi mphepo chabe?
27
Zoonadi inu mumapondereza ana amasiye, ndi kuŵaika pa malonda abwenzi anu omwe.
28
“Tsono mundiyang'anitsitse bwino! Sindikulankhula zabodza pamaso panu.
29
Chonde, feŵani mtima, musachite zosalungama. Musandiimbe mlandu, poti ndine wolungama.
30
Kodi mukuganiza kuti ndikulankhula zabodza? Monga ine sindingasiyanitse chabwino ndi choipa?”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42