bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 21
Job 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 22 →
1
Tsono Yobe adayankha kuti,
2
“Mumvetsere bwino zimene ndikulankhula, kunditonthoza mtima kwanu kukhale komweko basi.
3
Loleni ndilankhuleko, ndikatha kulankhula, munditonzeretonzere.
4
Kodi ine ndimadandaulira munthu? Tsono ndilekerenji kupsa mtima?
5
Mundipenye, ndipo mudabwe, mugwire dzanja pakamwa.
6
Ndikaganiza zimenezo, ndimachita mantha, ndimanjenjemera kwambiri.
7
“Kodi anthu oipa amakhaliranji moyo? Bwanji amafika mpaka ukalamba, ndi kusanduka amphamvu pa ulamuliro?
8
Amaona zidzukulu zao, ana ao amakula bwino iwo akupenya.
9
Mabanja ao amakhala pabwino opanda mantha, mkwapulo wa Mulungu suŵakhudza nkomwe.
10
Ng'ombe zao zamphongo zimabereketsa nthaŵi zonse, ng'ombe zao zazikazi sizipoloza.
11
Ana ao amaseŵera pa bwalo, namavinavina ngati anaankhosa.
12
Anawo amaimba, namaliza ng'oma ndi pangwe. Amakondwa pomva kulira kwa chitoliro.
13
Masiku ao amatha iwowo akukondwa, amatsikira ku manda mwamtendere.
14
“Anthuwo amauza Mulungu kuti, ‘Tichokereni! Sitifuna kudziŵa njira zanu.
15
Kodi Mphambeyo ndaninso kuti tizimtumikira? Timapindula chiyani tikamapemphera kwa Iye?’
16
Iwowo akuti amapambana chifukwa cha ntchito zao. Koma ineyo maganizo amenewo sindigwirizana nawo.
17
“Nkangati nyale ya oipa idazimapo? Nkangati tsoka limaŵagwera? Nkangati Mulungu amaŵakwiyira naŵalanga?
18
Nkangati amaŵachotsa ngati phesi louluka ndi mphepo, ngati mungu wouluzika ndi kamvulumvulu?
19
Paja amati, ‘Mulungu amalanga mwana chifukwa cha machimo a bambo wake.’ Ai, koma Mulungu aŵabwezere chilango ochimwawo, kuti adziŵedi kuti Mulungu ndiye amalanga ochimwa.
20
Zoonadi ochimwawo alangidwe ndithu, alaŵe ukali wa Mphambe.
21
Nanga kodi amalabadira chiyani za ana ao iyeyo atafa, chiŵerengero cha nthaŵi yake chitatha?
22
Kodi alipo wina woti angaphunzitse Mulungu nzeru, poti Iyeyo amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
23
Ena amafa ali olemera kwambiri, ali pabwino, ndi pa mtendere.
24
Ndi onenepa, thupi lao lili nenjenenje! Ndiponso ali ndi chuma chambiri.
25
Koma ena amafa mtima wao uli woŵaŵa, osalaŵapo chabwino chilichonse.
26
Koma olemera ndi osauka omwe onsewo amafa naikidwa m'manda, ndipo amagwa mphutsi.
27
“Ndikudziŵa zimene mukuganiza, ndikudziŵanso chiwembu chanu chimene mukuti mundichite.
28
Inu mumafunsana kuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti? Kodi hema limene munkakhala anthu oipa aja lili kuti?’
29
Kodi simudaŵafunsepo anthu oyenda mu mseu? Nanga kodi simuvomereza zimene iwowo amanena?
30
Pa tsiku lakuti Mulungu alanga anthu, munthu woipa salangidwa konse. Amapulumuka pa tsiku loonekera mkwiyo wa Mulungu.
31
Palibe ndi mmodzi yemwe amene amadzudzula munthu woipa, kapena kumbwezera zoipa zimene adachita.
32
Pamene aikidwa m'manda, anthu amachezera pa manda ake.
33
Anthu onse amatsatira mtembo wake. Amene amatsogola ndi osaŵerengeka, ndipo amakaika mtembo wakewo bwinobwino.
34
Nanga inu mudzandisangalatsa bwanji ndi mau opanda pake? Zimene mwayankhazi ndi mabodza okhaokha.” Elifazi
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42