bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 30
Job 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 31 →
1
“Koma tsopano akundiyesa chinthu chochiseka, anthu amene ali ana kwa ine, anthu oti ndi atate ao omwe sindikadaŵayesa oyenera kuti athandizane ndi agalu kuŵeta nkhosa zanga.
2
Kodi mphamvu zao zikadandipinduliranji, anthu amene nyonga zao zidatha kale?
3
Anali atatheratu kuwonda ndi njala, natsala mafupa okhaokha, ankakungudza nthaka youma yachipululu.
4
Ankathyola therere ndi masamba a zitsamba, ankadya mizu ya dinde.
5
Ankaŵapirikitsa pakati pa anthu, anzao ankaŵakuwa ngati mbala.
6
Ankaumirizidwa kumakhala m'zigwembe za mitsinje, m'maenje am'nthaka ndi am'matanthwe.
7
Ankalira ngati nyama kuthengo, ndipo ankaunjikana pamodzi pa zitsamba zaminga.
8
Iwowo anali opusa, achabechabe okhaokha, ndipo adaŵachotsa m'dziko.
9
“Tsopano ine ndasanduka nyimbo yao, ndasanduka chisudzo chao.
10
Ineyo ndimaŵanyansa, ndipo amandithaŵa. Akangondiwona, salephera kuti malovu nzee m'maso mwangamu.
11
Poti Mulungu adandifooketsa ndi kundichepetsa, iwowo adalekeratu kundiwopa.
12
Ku dzanja langa lamanja anthu achiwawa akundiwukira, akukumba mbuna yoti ndigweremo, akukonzekera njira zondiwonongeratu.
13
Akunditsekera njira, ndipo akufuna kundichititsa ngozi, palibe wina aliyense woŵaletsa.
14
Akundithamangira ngati madzi oloŵera pa linga logumuka, akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.
15
Zoopsa zandigwera. Ulemu wanga wachita ngati kuuluzika ndi mphepo, chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.
16
“Tsopano mtima wanga wachokamo. Ndili pa mavuto, ndilibe popumira.
17
Mafupa anga akuphwanya usiku, zoŵaŵa sizikuleka.
18
Chovala changa chakwinyikakwinyika chifukwa cha matenda, chikundithina ngati khosi la mkanjo wanga.
19
Mulungu wandiponya m'matope, ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.
20
“Ndimalira kwa Inu Mulungu, koma simundiyankha. Ndimapemphera, koma inu simundiyang'anako.
21
Inu mwandichita zankhanza, mwandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.
22
Inu mwandiika pa mphepo, mwandinyamula ndi mphepoyo, ndipo mwandiponya mu mkuntho wa namondwe.
23
Tsono ndikudziŵa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa yanga, kumene aliyense adzapitako.
24
“Komabe kodi munthu wam'mazunzo satambalitsa dzanja? Kodi salira chithandizo m'mavuto mwakemo?
25
Kodi ine sindidalire nawo anzanga amene anali pa mavuto? Kodi mtima wanga sudaŵamvere chisoni anthu osauka?
26
Koma pamene ndinkayembekeza zabwino, zovuta ndiye zimene zidandigwera. Pamene ndinkayembekeza kuŵala, mdima ndi umene udandiphimba.
27
Mtima wanga ukuŵaŵa, ndikusoŵa mpumulo, masiku onse ndili pa mavuto.
28
Ndikuyenda mu mdima popanda dzuŵa konse. Komabe ndimaimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira.
29
Kulira kwanga kuli ngati kwa nkhandwe, ndimakhala ndekha ngati nthiŵatiŵa.
30
Khungu langa likuyamba kuda ndi kunyenyeka, Mafupa anga akutentha ndi chitungu.
31
Pangwe wanga wasanduka woimbira maliro, chitoliro changa chikupolokeza anthu olira.” Yobe avomera kuchimwa kwake.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42