bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Job 37
Job 37
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 38 →
1
Nanenso ndimaopa zazikuluzi, mtima wanga umalumphalumpha kuchoka m'malo mwake.
2
Mumvetsetse kulira kwa liwu la Mulungu, ndiye kuti kugunda kotuluka m'kamwa mwake.
3
Amaponya ching'aning'ani pansi pa thambo, kuŵala kwake kumafika ku ngodya zonse za dziko lapansi.
4
Pambuyo pake kugunda kwa Mulungu kumamveka, amagunda ndi liwu lake lalikulu pamene mphezi zikung'anipa.
5
Mulungu amachita zodabwitsa ndi liwu lake. Amachita zazikulu zimene sitingathe kumvetsa.
6
Amalamula chisanu chambee kuti chigwe pa dziko lapansi. Amalamulanso mvula kuti igwe mwamphamvu.
7
Pamenepo Mulungu amalepheretsa anthu kugwira ntchito zao. Motero iwowo amazindikira kuti Iye mwini ali pa ntchito.
8
Pomwepo zilombo zimathaŵira ku michembo yake, ndipo zimakabisalira m'ngaka zake.
9
Kamvulumvulu amakuntha kuchokera ku malo ake, mphepo imadzetsa chisanu chambiri.
10
Mpweya wa Mulungu umaunditsa chisanu, ndipo madzi am'nyanja amauma kuti gwa.
11
Mitambo yochindikira amaidzaza ndi madzi a mvula, ndipo amabalalitsa zing'aning'ani kuchokera m'mitambo.
12
Mulungu amayendetsa mitambo mozungulirazungulira, kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.
13
Mwina amagwetsa mvula pansi pano kuti ikhale chilango, mwina kuti aonetse chikondi kwa anthu, pothirira nthaka yao.
14
“Inu aYobe, tamvani izi, imani, muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.
15
Kodi mukudziŵa m'mene Mulungu amazichitira, ndi m'mene amang'anipitsira mphezi m'mitambo yake?
16
Kaya mukudziŵa m'mene Mulungu amayalira mitambo, ntchito yosonyeza nzeru zake zodabwitsa,
17
paja inu zovala zanu mumamva kutentha kwambiri pamene mphepo yakumwera ikuwomba pa dziko?
18
Kodi mungathe kufanafana naye Mulungu amene adatambasula thambo lili lolimba ngati chitsulo?
19
“Chabwino, tiphunzitsenitu zoti tidzamuuze. Ifeyo sitingathe kunena kanthu poti mwa ife mwachita mdima.
20
Kodi nkofunikira kumdziŵitsa Mulungu kuti ndili naye ndi mau? Kodi kutero si kuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?
21
“Tsopano anthu sangathe kuyang'anitsitsa kuŵala, pamene kukunyezimira kwambiri mu mlengalenga, pamene mphepo yaomba nkuchotsa mitambo yonse.
22
Kuŵala kwake kumaonekera chakumpoto. Mulungu amaonetsa ulemerero woopsa.
23
Mphambe sitingathe kumufika pafupi, ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu. Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu.
24
Nchifukwa chake anthu amamuwopa kwambiri. Iye sasamalako wina aliyense amene amadzinyenga kuti ndi wanzeru.” Chauta alankhula.
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 38 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42